1 Ndipo zinatha kupangidwa zakumwamba ndi dziko lapansi, ndi khamu lao lonse.
2 Tsiku lacisanu ndi ciwiri Mulungu anamariza nchito yonse anaipanga; ndipo anapuma tsiku lacisanu ndi ciwiri ku nchito yace yonse.
3 Mulungu ndipo anadalitsa tsiku lacisanu ndi ciwiri, naliyeretsa limenelo: cifukwa limenelo ada puma ku nchito yace yonse imene Mulungu anailenga ndi kupanga.
4 Imeneyo ndiyo mibadwo yao ya zakumwamba ndi dziko lapansi, pamene zinalengedwa, tsiku lomwe Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zakumwamba.
5 Ndi zomera zonse za m'munda zisanakhale m'dziko lapansi, ndiponso matherere onse a m'munda asanamere; cifukwa Yehova Mulungu sanabvumbitsire mvula pa dziko lapansi, ndipo panalibe munthu wakulima nthaka;
6 kama inakwera nkhungu yoturuka pa dziko lapansi, niithirira ponse pamwamba pa nthaka.
7 Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwace; munthuyo nakhala wamoyo.
8 Ndipo Yehova Mulungu anabzala m'munda ku Edene cakum'mawa; momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo.
9 Ndipo Yehova Mulungu anameretsa m'nthaka mitengo yonse yokoma m'maso ndi yabwino kudya; ndiponso mtengo wa moyo pakati pa mundapo, ndi mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa.
10 Ndipo unaturuka m'Edene mtsinje wakuthirira m'mundamo, m'menemo ndipo unalekana nucita miyendo inai.
11 Dzina la wakuyamba ndi Pisoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Havila, m'mene muli golidi;
12 golidi wa dziko ali wabwino; ndimonso muli bedola ndi mwala wasohamu.
13 Dzina la mtsinje waciwiri ndi Gihoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Kusi.
14 Dzina la mtsinje wacitatu ndi Hidikeli: umenewo ndiwo wakuyenda ca kum'mawa kwace kwa Asuri. Mtsinje wacinai ndi Pirate.
15 Ndipo Yehova Mulungu anatenga munthuyo, namuika iye m'munda wa Eriene kuti aulime nauyang'anire.
16 Ndipo Yehova Mulungu anamuuza munthuyo, nati, Mitengo yonse ya m'munda udyeko;
17 koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa, usadye umenewo; cifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.
18 Yehova Mulungu ndipo anati, Si kwabwino kuti munthuakhale yekha; ndidzampangira womthangatira iye.
19 Ndipo Yehova Mulungu anaumba ndi nthaka zamoyo zonse za m'thengo, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga; ndipo anapita nazo kwa Adamu kuti aone maina omwe adzazicha; ndipo maina omwe onse anazicha Adamu zamoyo zonse, omwewo ndiwo maina ao.
20 Adamu ndipo anazicha maina zinyama zonse, ndi mbalame za m'mlengalenga ndi zamoyo zonse za m'thengo: koma kwa Adamu sanapezedwa womthangatira iye.
21 Koma Yehova Mulungu anamgonetsa Adamu tulo tatikuru, ndipo anagona: ndipo anatengako nthiti yace imodzi, natsekapo ndi mnofu pamalo pace:
22 ndipo nthitiyo anaicotsa Yehova Mulungu mwa Adamu anaipanga mkazi, ndipo ananka naye kwa Adamu.
23 Ndipo anati Adamu, Uyu tsopano ndiye pfupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga; ndipo adzachedwa Mkazi, cifukwa anamtenga mwa mwamuna.
24 Cifukwa cotero mwamuna adzasiya atate wace ndi amace nadzadziphatika kwa mkazi wace: ndipo adzakhala thupi limodzi.
25 Onse awiri ndipo anali amarisece, mwamuna ndi mkazi wace, ndipo analibe manyazi.