Genesis 30 BL92

1 Pamene Rakele anaona kuti sanambalira Yakobo ana, Rakele anamcitira mkuru wace nsanje; nati kwa Yakobo, Ndipatse ana ndingafe.

2 Ndipo Yakobo anapsa mtima ndi Rakele; nati, Kodi ine ndikhala m'malo a Mulungu amene akukaniza iwe zipatso za mimba?

3 Ndipo Rakele anati, Taonani mdzakazi wanga Biliha, mulowe kwa iye; ndipo iye adzabala pa maondo anga, kuti inenso ndionerepo ana pa iye.

4 Ndipo Rakele anampatsa iye Biliha mdzakazi wace akhale mkazi wace; ndipo Yakobo analowa kwa iye.

5 Ndipo Biliha anatenga pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna.

6 Rakele ndipo anati, Mulungu wandiweruzira ine, namva mau anga, nandipatsa ine mwana; cifukwa cace anamucha dzina lace Dani.

7 Ndipo Biliha mdzakazi wace wa Rakele anatenganso pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna waciwiri.

8 Ndipo Rakele anati, Ndi malimbano a Mulungu ndalimbana naye mkuru wanga, ndipo ndapambana naye; ndipo anamucha dzina lace Nafitali.

9 Pamene Leya anaona kuti analeka kubala, anatenga Zilipa mdzakazi wace, nampatsa iye kwa Yakobo kuti akhale mkazi wace.

10 Ndipo Zilipa mdzakazi wace wa Leya anambalira Yakobo mwana wamwamuna.

11 Ndipo Leyaanati, Wamwai ine! ndipo anamucha dzina lace Gadi.

12 Ndipo Zilipa mdzakazi wa Leya anambalira Yakobo mwana wamwamuna waciwiri.

13 Ndipo Leya anati, Ndakondwa inel cifukwa kuti ana akazi adzandicha ine wokondwa: ndipo anamucha dzina lace Aseri.

14 Ndipo Rubeni ananka masiku akudula tirigu, napeza zipatso za mankhwala a cikondi m'thengo, nazitengera kwa amace Leva, Ndipo Rakele anati kwa Leya, Undipatseko mankhwala a mwana wako.

15 Ndipo iye anati kwa Rakele, Kodi mpacabe kuti iwe wacotsa mwamuna wanga? Kodi ufuna kucotsanso mankhwala a mwana wanga? Rakele ndipo anati, Cifukwa cace iye adaagona nawe usiku uno cifukwa ca mankhwala a mwana wako.

16 Ndipo Yakobo anadza madzulo kucokera kumunda, ndipo Leya ananka kukomana naye, nati, Ulowe kwa ine cifukwa ndakulipilira iwe ndi mankhwala a mwana wanga. Ndipo anagona naye usiku womwewo.

17 Ndipo Mulungu anamvera Leya, ndipo anatenga pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna wacisanu.

18 Ndipo Leya anati, Mulungu wandipatsa ine mphotho yanga, cifukwa ndapatsa mdzakazi wanga kwa mwamuna wanga: namucha dzina lace lsakara.

19 Ndipo Leya anatenganso pakati nambalira Yakobo mwana wamwamuna wacisanu ndi cimodzi.

20 Ndipo Leya anati, Mulungu anandipatsa ine mphatso yabwino; tsopane mwamuna wanga adzakhala ndi ine, cifukwa ndambalira iye ana amuna asanu ndi mmodzi; ndipo anamucha dzina lace Zebuloni.

21 Pambuyo pace ndipo anabala mwana wamkazi, namucha dzina lace Dina.

22 Ndipo Mulungu anakumbukila Rakele, ndipo Mulungu anamvera iye, natsegula m'mimba mwace.

23 Ndipo anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, nati, Mulungu wacotsa manyazi anga;

24 namucha dzina lace Yosefe; ndipo anati, Yehova anandionjezera ine mwana wamwamuna wina.

Laban; apangana ndi Yakobo

25 Ndipo panali pamene Rakele anabala Yosefe, Yakobo anati kwa Labani, Undisudzule ine ndinke kwathu ku dziko langa.

26 Undipatse ine akazi anga ndi ana anga cifukwa ca iwowa ndakutumikira iwe, ndimuke: cifukwa udziwa iwe nchito imene ndinakugwirira iwe.

27 Ndipo Labani anati kwa iye, Ngatitu ndikapeza ufulu pamaso pako, ukhale, cifukwa ndazindikira kuti Yehova wandidalitsa ine cifukwa ca iwe.

28 Ndipo iye anati, Undipangire ine malipiro ako, ndipo ndidzakupatsa.

29 Ndipo iye anati kwa Labani, Udziwa iwe comwe ndakutumikira iwe ndi comwe zacita zoweta zako ndi ine.

30 Cifukwa ndisadafike ine, iwe unali nazo zowerengeka, ndipo zacuruka zambirimbiri; Yehova wakudalitsa iwe kuli konse ndinayendako: tsopano ndidzamanga liti banja langa?

31 Ndipo iye anati, Ndikupatsa iwe bwanji? Ndipo Yakobo anati, Usandipatse ine kanthu; ukandicitira ine cotero, ine ndidzadyetsanso ndi kusunganso ziweto zako.

32 Ndidzapita ine lero pakati pa ziweto zonse ndi kusankhasankha m'menemo zoweta zonse zamathotho-mathotho ndi zamaanga-maanga, ndi za nkhosa zonse, ndi mbuzi zonse zamaangamaanga ndi zamathotho-mathotho: zotero zidzakhala malipiro anga.

33 Cotero cilungamo canga cidzandibvomereza m'tsogolomo, pamene udzandifika cifukwa ca malipiro amene ali patsogolo pako; iri yonse yosakhala yamathotho-mathotho ndi yamaanga-maanga ya mbuzi, ndi iri yonse ya mbuzi yosakhala yakuda, ikapezedwa ndi ine, udzaiyesa yakuba.

34 Ndipo Labani anati, Taona, kukhale monga mau ako.

35 Tsiku lomwelo Labani anacotsa atonde amene anali amipyololo-mipyololo ndi amathotho-mathotho, ndi mbuzi zazikazi zinali zamaanga-maanga ndi zamathotho-mathotho zonse zinali zoyera pang'ono, ndi zakuda zonse za nkhosa, napatsa m'dzanja la ana ace amuna.

36 Ndipo iye yekha anatalikitsana ndi Yakobo ulendo wa masiku atatu: ndipo Yakobo anadyetsa ziweto zina za Labani.

37 Ndipo Yakobo anatenga nthyole za mtengo wowisi walibne, ndi za mtengo wakatungurume, ndi za mtengo waarimoni, nakupula m'menemo mizere yoyera, naonetsa moyera mwa m'nthyolemo.

38 Ndipo anaimitsa nthyole zimene anazikupula pandunji ndi zoweta m'micera yakumwera, m'mene ziweto zinafika kumweramo, ndipo zidatenga mabere pamene zinadza kumwa.

39 Ndipo ziweto zinatenga mabere patsogolo pa nthyolezo, ndipo zoweta zinabala zamipyololomipyololo, ndi mathotho-mathotho, ndi zamaanga-maanga.

40 Ndipo Yakobo analekanitsa ana a nkhosa naziika nkhope za zoweta kuti ziyang'anire zamipyololo-mipyololo, ndi zakuda zonse za m'zoweta za Labani, ndipo anaika magulu ace pa okha; sanaziika pa zoweta za Labani.

41 Ndipo panali pamene zoweta zolimba zidatenga mabere, Yakobo anaika nthyole pamaso pa zoweta m'miceramo kuti zitenge mabere pa nthyolezo.

42 Koma pamene ziweto zinali zofoka, sanaziika zimenezo: ndipo zofoka zinali za Labani, ndi zolimba zinali za Yakobo.

43 Munthuyo ndipo anakula kwambiri, nali nazo zoweta zambiri, ndi akapolo amuna ndi akazi, ndi ngamila, ndi aburu.