Genesis 3 BL92

Kucimwa kwa Adamu ndi Hava

1 Ndipo njoka inali yakucenjera yoposa zamoyo zonse za m'thengo zimene anazipanga Yehova Mulungu, Ndipo inati kwa mkaziyo, Ea! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m'mundamu?

2 Mkaziyo ndipo anati kwa njoka, Zipatso za mitengo ya m'mundamu tidye.

3 Koma zipatso za mtengo umene uti m'kati mwa munda, Mulungu anati, Musadye umenewo, musakhudze umenewo, mungadzafe.

4 Njokayo ndipo inati kwa mkaziyo, Kufa simudzafai;

5 cifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.

6 Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m'maso, mtengo wolakalakika wakupatsa nzeru, anatenga zipatso zace, nadya, napatsanso mwamuna wace amene ali nave, nadya iyenso,

7 Ndipo anatseguka maso ao a onse awiri, nadziwa kuti anali amarisece: ndipo adasoka masamba amkuyu, nadzipangira mateweta.

8 Ndipo anamva mau a Yehova Mulungu alinkuyendayenda m'munda nthawi yamadzulo: ndipo anabisala Adamu ndi mkazi wace pamaso pa Yehova Mulungu pakati pa mitengo ya m'munda.

9 Ndipo Yehova Mulungu anaitana mwamunayo nati kwa iye, Uli kuti?

10 Ndipo anati, Ndinamva mau anu m'mundamu, ndipo ndinaopa cifukwa ndinali wamarisece ine; ndipo ndinabisala.

11 Ndipo anati, Ndani anakuuza iwe kuti uli wamarisece? Kodi wadya za mtengo uja, umene ndinakuuza iwe kuti usadye?

12 Ndipo anati mwamunayo, Mkazi amene munandipatsa ine kuti akhale ndi ine, ameneyo anandipatsa ine za mtengo, ndipo ndinadya.

13 Ndipo Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, Ciani cimene wacitaci? Ndipo anati mkaziyo, Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.

14 Ndipo anati Yehova Mulungu kwa njokayo, Cifukwa kuti wacita ici, wotembereredwa ndiwe wopambana ndi zinyama zonse ndi zamoyo zonse za m'thengo: uziyenda ndi pamimba pako, uzidya pfumbi masiku onse a moyo wako:

15 ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yace; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira citende cace.

16 Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzacurukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.

17 Kwa Adamu ndipo anati, Cifukwa kuti wamvera mau a mkazi wako, nudya za mtengo umene ndinakuuza iwe kuti, Usadyeko; nthaka ikhale yotembereredwa cifukwa ca iwe; m'kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako:

18 minga ndi mitula idzakubalira iwe; ndipo udzadya therere la m'thengo:

19 m'thukuta la nkhope yako udzadya cakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: cifukwa kuti m'menemo unatengedwa: cifukwa kuti ndiwe pfumbi, ndi kupfumbiko udzabwerera.

20 Ndipo mwamuna anamucha dzina la mkazi wace, Hava; cifukwa ndiye amace wa amoyo onse.

21 Yehova Mulungu ndipo anapangira Adamu ndi mkazi wace maraya azikopa, nawabveka iwo.

22 Ndipo anati Yehova Mulungu, Taonani, munthuyo akhala ngati mmodzi wa ife, wakudziwa zabwino ndi zoipa: ndipo tsopano kuti asatambasule dzanja lace ndi kutenga za mtengo wa moyo, ndi kudya, ndi kukhala ndi moyo nthawi zonse,

23 Yehova Mulungu anamturutsa iye m'munda wa Edene, kuti alime nthaka m'mene anamtenga iye.

24 Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazika Makerubi ca kum'mawa kwace kwa munda wa Edene, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.