Genesis 40 BL92

Yosefe m'kaidi amasulira maloto

1 Ndipo panali zitapita izi, wopereka cikho wa mfumu ya Aigupto ndi wophika mkate wace anamcimwira mbuye wao mfumu ya Aigupto.

2 Ndipo Farao anakwiyira akuru ace awiriwo wamkuru wa opereka cikho, ndi wamkuru wa ophika mkate.

3 Ndipo anaika iwo asungidwe m'nyumba ya kazembe wa alonda, m'kaidi, umo anamangidwa Yosefe.

4 Ndipo kazembe wa alonda anapereka iwo kwa Yosefe, ndipo iye anawatumikira iwo: ndipo anakhala nthawi mosungidwamo.

5 Ndipo analota maloto onse awiri, yense lata lace, usiku umodzi, yense monga mwa kumasulira kwa loto lace, wopereka cikho ndi wophika mkate wa mfumu ya Aigupto, amene anamangidwa m'kaidi.

6 Ndipo Yosefe analowa kwa iwo m'mawa, nawaona iwo, taonani, anali oziya.

7 Ndipo anafunsa akuru a Farao osungidwa naye m'nyumba ya mbuyace, kuti, Nkhope zanu zagwa bwanji lero?

8 Ndipo iwo anati kwa iye, Ife talota maloto, ndipo tiribe wotimasulira. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Kodi Mwini kumasulira si ndiye Mulungu? Mundifotokozeretu.

9 Ndipo wopereka cikho wamkuru anafotokozera Yosefe loto lace, nati kwa iye, M'kulota kwanga, taona, mpesa unali pamaso panga:

10 ndipo m'mpesamo munali nthambi zitatu: ndipo unali wonga unaphuka, ndipo maluwa ace anaphuka; nabala matsamvu ace mphesa zakuca:

11 ndipo cikho ca Farao cinali m'dzanjalanga: ndipo ndinatenga mphesa, ndi kufinyira m'cikho ca Farao ndi kupereka cikho m'dzanja la Farao.

12 Ndipo Yosefe anati kwa iye, Mmasuliro wace ndi uwu: nthambi zitatu ndizo masiku atatu;

13 akali masiku atatu Farao adzatukula mutu wako, nadzabwezera iwe nchito yako; ndipo udzapereka cikho ca Farao m'dzanja lace, monga kale lomwe m'mene unali wopereka cikho cace.

14 Koma undikumbukire ine m'mene kudzakhala bwino ndi iwe, ndipoundicitiretu ine kukoma mtima: nundichule ine kwa Farao, nunditurutse ine m'nyumbamu:

15 cifukwa kuti ndinabedwa ndithu m'dziko la Ahebri; ndiponso pano sindinacite kanthu kakundiikira ine m'dzeniemu.

16 Pamene wophika mkate anaona kuti mmasuliro wace unali wabwino, iye anati kwa Yosefe, Inenso ndinalimkulota, ndipo, taonani, malicero atatu a mikate yoyera anali pamtu panga;

17 m'licelo lapamwamba munali mikate ya Farao ya mitundu mitundu; ndipo mbalame zinadya ya m'licelo la pamutu panga.

18 Ndipo Yosefe anayankha nati, Mmasuliro wace ndi uwu: malicelo atatu ndiwo masiku atatu;

19 akali masiku atatu Farao adzakweza mutu wako ndi kuucotsa, nadzakupacika iwe pamtengo: ndipo mbalame zidzadya mnofu wako.

20 Ndipo panali tsiku lacitatu ndilo tsiku lakubadwa kwace kwa Farao, iye anakonzera anyamata ace madyerero, ndipo anakweza mutu wa wopereka cikho wamkuru, ndi mutu wa wophika mkate wamkuru pakati pa anyamata ace.

21 Ndipo anabwezanso wopereka cikho ku nchito yace; ndipo iye anapereka cikho m'manja a Farao.

22 Koma anampacika wophika mkate wamkuru; monga Yosefe anawamasulira.

23 Koma wopereka cikho wamkuru sanakumbukira Yosefe, koma anamuiwala.