Genesis 10 BL92

Mbumba ya Nowa

1 Mibadwo ya ana a Nowa, Semu, Hamu, ndi Yafeti, ndi iyi; kwa iwo ndipo kunabadwa ana amuna, citapita cigumula cija.

2 Ana amuna a Yafeti: Gomeri, ndi Magogi, ndi Madai, ndi Yavani, ndi Tubala, ndi Mesheki, ndi Tirasi,

3 Ndi ana amuna a Gomeri: Asekenazo, ndi Rifata, ndi Togarma.

4 Ndi ana amuna a Yavani: Elisa, ndi Tarisisi, ndi Kitimu, ndi Dodanimu.

5 Amenewo ndipo anagawa zisi za amitundu m'maiko mwao, onse amene monga mwa cinenedwe cao; ndi mwa mabanja ao, ndi m'mitundu yao.

6 Ndi ana amuna a Hamu: Kusi, ndi Mizraimu, ndi Puti, ndi Kanani.

7 Ndi ana amuna a Kusi: Seba, ndi Havila, ndi Sabita, ndi Raama, ndi Sabiteka; ndi ana a Raama: Sheba ndi Dedane.

8 Ndipo Kusi anabala Nimrode; ndipo iye anayamba kukhala wamphamvu pa dziko lapansi.

9 Iye ndiye mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova: cifukwa cace kunanenedwa, Monga Nimrode mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova.

10 Ndipo kuyamba kwace kwa ufumu wace kunali Babele, ndi Ereke, ndi Akadi, ndi Kaline, m'dziko la Sinara.

11 M'dziko momwemo iye anaturuka kunka ku Ashuri, namanga Nineve, ndi mudzi wa Rehoboti, ndi Kala,

12 ndi Resene pakati pa Nineve ndi Kala: umenewo ndi mudzi waukuru.

13 Mizraimu ndipo anabala Ludimu, ndi Anamimu, ndi Lehabimu, ndi Nafituhimu,

14 ndi Patrusimu, ndi Kasiluhimu, m'menemo ndipo anaturuka Afilisti, ndi Kafitorimu.

15 Ndipo Kanani anabala Sidoni woyamba wace, ndi Heti:

16 ndi Ajebusi, ndi Aamori, ndi Agirigasi;

17 ndi Ahivi, ndi Aariki, ndi Asini;

18 ndi Aaravadi, ndi Aazemari, ndi Ahamati; pambuyo pace pamenepo ndipo mabanja a Akanani anafalikira.

19 Ndipo malire a Akanani anayamba pa Sidoni, pakunka ku Gerari ndi ku Gaza; pakunka ku Sodomu, ndi ku Gomora, ndi Adima, ndi Zeboimu, kufikira ku Lasa.

20 Amenewa ndi ana amuna a Hamu monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao.

21 Ndiponso kwa Semu atate wa ana onse a Ebere, mkuru wa Yafeti, kwa iye kunabadwa ana.

22 Ana amuna a Semu; Elamu, ndi Ashuri, ndi Aripakasadi, ndi Ludi, ndi Aramu.

23 Ndi ana a Aramu: Uzi ndi Huli, ndi Getere, ndi Masi.

24 Aripakasadi ndipo anabala Sela; ndipo Sela anabala Ebere.

25 Kwa Ebere ndipo kunabadwa ana amuna awiri; dzina la wina ndi Pelege; cifukwa kuti m'masiku ace dziko lapansi linagawanikana; dzina la mphwace ndi Yokitani.

26 Ndipo Yokitani anabala Alamodadi, ndi Selefe, ndi Hazaramaveti, ndi Yera;

27 ndi Hadorimu ndi Uzali, ndi Dikila;

28 ndi Obali, ndi Abimaele, ndi Sheva;

29 ndi Ofiri ndi Havila, ndi obabi; onse amenewa ndi ana a okitani.

30 Kwao kunayamba pa Mesa pakunka ku Sefere phiri la kum'mawa.

31 Amenewa ndi ana a Semu, monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao.

32 Amenewo ndi mabanja a ana a Nowa monga mwa mibadwo yao, m'mitundu yao: ndi amenewo anagawanika mitundu pa dziko lapansi, citapita cigumula.