Genesis 5 BL92

Mbumba ya Seti

1 Ili ndi buku la mibadwo ya Adamu. Tsiku lomwe Mulungu analenga munthu anamlenga m'cifanizo ca Mulungu;

2 anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nawadalitsa iwo nacha mtundu wao anthu, tsiku lomwe anawalenga iwo.

3 Ndipo Adamu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza makumi atatu, nabala mwana wamwamuna m'cifanizo cace; namucha dzina lace Seti.

4 Masiku ace Adamu atabala Seti, anali zaka mazana asanu ndi atatu; ndipo anabala ana amuna ndi akazi.

5 Masiku ace onse anakhala ndi moyo Adamu anali zaka mazana asanu ndi anai, kudza makumi atatu; ndipo anamwalira.

6 Ndipo Seti anakhala ndi moyo zaka zana kudza zisanu, nabala Enosi;

7 ndipo Seti anakhala ndi moyo, atabala Enosi, zaka mazana asanu ndi atatu kudza zisanu ndi ziwiri: ndipo anabala ana amuna ndi akazi:

8 masiku ace onse a Seti anali zaka mazana asanu ndi anai kudza khumi ndi ziwiri; ndipo anamwalira.

9 Ndipo Enosi anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi anai, nabala Kenani;

10 ndipo anakhala ndi moyo Enosi, atabala Kenani, zaka mazana asanu ndi atatu kudza khumi ndi zisanu: ndipo anabala ana amuna ndi akazi.

11 Masiku ace onse a Enosi anali mazana asanu ndi anai kudza zisanu; ndipo anamwalira.

12 Ndipo Kenani anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi awiri, ndipo anabala Mahalalele:

13 ndipo Kenani anakhala ndi moyo, atabala Mahalalele zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi anai, ndipo anabala ana amuna ndi akazi;

14 masiku ace onse a Kenani anali zaka mazana asanu ndi anai kudza khumi; ndipo anamwalira.

15 Ndipo Mahalalele anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu, nabala Yaredi;

16 ndipo Mahalalele anakhala ndi moyo, atabala Yaredi, zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi atatu, nabala ana amuna ndi akazi:

17 masiku ace onse a Mahalalele anali zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi asanu ndi anai ndi zisanu; ndipo anamwalira.

18 Ndipo Yaredi anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi limodzi ndi ziwiri, nabala Enoke;

19 ndipo Yaredi anakhala ndi moyo, atabala Enoke, zaka mazana asanu ndi atatu, nabala ana amuna ndi akazi;

20 masiku ace onse a Yaledi anali zaka mazana asanu ndi anai kudza maitumi asanu ndi limodzi ndi ziwiri: ndipo anamwalira.

21 Ndipo Enoke anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu, nabala Metusela:

22 ndipo Enoke anayendabe ndi Mulungu, atabala Metusela, zaka mazana atatu, nabala ana amuna ndi akazi;

23 masiku ace onse a Enoke anali mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi ndi zisanu;

24 ndipo Enoke anayendabe ndi Mulungu; ndipo panalibe iye; pakuti Mulungu anamtenga.

25 Ndipo Metusela anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi atatu ndi zisanu ndi ziwiri, nabala Lameke;

26 ndipo Metusela anakhala ndi moyo, atabala Lameke, zaka mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi atatu ndi ziwiri, nabala ana amuna ndi akazi:

27 masiku ace onse a Metusela anali mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi zinai; ndipo anamwalira.

28 Ndipo Lameke anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi atatu ndi ziwiri, nabala mwana wamwamuna;

29 namucha dzina lace Nowa, ndi kuti, Yemweyu adzatonthoza mtima wathu pa nchito zathu zobvuta za manja athu, cifukwa ca nthaka imene anaitemberera Yehova;

30 ndipo Lameke anakhala ndi moyo atabala Nowa, zaka mazana asanu kudza makumi asanu ndi anai ndi zisanu, nabala ana amuna ndi akazi:

31 masiku ace onse a Lameke anali zaka mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi awiri; ndipo anamwa lira.

32 Ndipo Nowa anali wa zaka mazana asanu; ndipo Nowa anabala Semu ndi Hamu ndi Yafeti.