Genesis 45 BL92

Yosefe adziulula kwa abale ace

1 Ndipo Yosefe sanakhoza kudziletsa pamaso pa onse amene anaima naye: nati, Turutsa anthu onse pamaso panga. Ndipo panalibe munthu pamodzi ndi iye pamene Yosefe anadziululira yekha kwa abale ace.

2 Ndipo analira momveka, ndipo anamva Aaigupto, ndipo anamva a m'nyumba ya Farao.

3 Ndipo Yosefe anati kwa abale ace, Ine ndine Yosefe; kodi-akali ndi moyo atate wanga? Ndipo abale ace sanakhoza kumyankha iye; pakuti anabvutidwa pakumuona iye.

4 Ndipo Yosefe anati kwa abale ace, Muyandikiretu kwa ine; nayandikira. Ndipo iye anati, Ine ndine Yosefe mbale wanu, ine ndemwe munandigulitsa ndilowe m'Aigupto.

5 Tsopano musaphwetekwe mtima, musadzikwiyira inu nokha, kuti munandigulitsira ine kuno, pakuti Mulungu ananditumiza ine patsogolo panu kuti ndisunge moyo.

6 Zaka ziwirizi muli njala m'dziko muno; ndipo zatsala zaka zisanu, zopanda kulima kapena kusenga,

7 Ndipo Mulungu anatumiza ine patsogolo panu kuti ndikhazike inu mutsale m'dziko lapansi, ndi kusunga inu amoyo ndi cipulumutso cacikuru.

8 Ndipo tsopano sindinu amene munanditumiza ine ndifike kuno, koma Mulungu, ndipo anandiyesa ine atate wa Farao, ndi mwini banja lace lonse, ndi wolamulira dziko lonse la Aigupto.

9 Fulumirani, kwerani kunka kwa atate wanga, muti kwa iye, Cotere ati Yosefe mwana wanu, Mulungu wandiyesa ine mwini Aigupto lonse: tsikirani kwa ine, musacedwe.

10 Ndipo mudzakhala m'dziko la Goseni, mudzakhala pafupi ndi ine, inu ndi ana anu, ndi ana a ana anu, ndi nkhosa zanu, ndi zoweta zanu, ndi zonse muli nazo;

11 ndipo ndidzacereza inu komweko; pakuti zatsala zaka zisanu za njala; kuti mungafikire umphawi, inu ndi banja lanu, ndi onse muli nao.

12 Taonani, maso anu aona, ndi maso a mphwanga Benjamini, kuti ndi m'kamwa mwanga ndirikulankhula ndi inu.

13 Ndipo mudzafotokozera atate wanga za ulemerero wanga wonse m'Aigupto, ndi zonse mwaziona; ndipo muzifulumira ndi kutsitsira kuno atate wanga.

14 Ndipo anagwa pakhosi pace pa Benjamini, nalira; ndipo Benjamini nalira pakhosi pace.

15 Ndipo anampsompsona abale ace onse, nalilira iwo; ndipo pambuyo pace abale ace onse anaceza naye.

16 Ndipo mbiri yace inamveka m'nyumba ya Farao, kuti abale ace a Yosefe afika; ndipo inamkomera Farao, ndi anyamata ace.

17 Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Nena ndi abale ako, Citani ici; senzetsani nyama zanu, ndi kupita kunka ku dziko la Kanani;

18 katengeni atate wanu ndi mabanja anu, nimudze kwa ine; ndipo ndidzakupatsani inu zabwino za dziko la Aigupto, ndipo mudzadya zonenepa za dzikoli.

19 Tsopano mwalamulidwa citani ici; muwatengere ana anu ndi akazi magareta a m'dziko la Aigupto; nimubwere naye atate wanu.

20 Musasamalire cuma canu; popeza zabwino za dziko lonse la Aigupto ndi zanu.

21 Ndipo ana a Israyeli anacita cotero: ndipo Yosefe anawapatsa iwo magareta monga analamulira Farao, nawapatsa phoso la panjira,

22 Onse anawapatsa yense zobvala zopindula; koma Benjamini anampatsa ndalama zasiliva mazana atatu ndi zobvala zopindula zisanu.

23 Kwa atate wace anatumiza zotere: aburu khumi osenza zinthu zabwino za m'Aigupto, ndi aburu akazi khumi osenza tirigu, ndi cakudya, ndi phoso la atate la panjira.

24 Ndipo anamukitsa abale ace, ndipo anacoka; ndipo anati kwa iwo, Musakangane panjira.

25 Ndipo anakwera kuturuka m'Aigupto, nafika ku dziko la Kanani kwa Yakobo atate wao.

26 Ndipo anamfotokozera iye kuti, Yosefe akali ndi moyo, ndipo alamulira m'dziko lonse la Aigupto, Pamenepo mtima wace unakomoka, pakuti sanawakhulupirira iwo.

27 Ndipo anamfotokozera iye mau onse a Yosefe amene ananena ndi iwo; ndipo pamene anaona magareta amene Yosefe anatumiza kuti amtengeremo, mtima wa Yakobo atate wao unatsitsimuka;

28 ndipo Israyeli anati, Cakwana; Yosefe mwana wanga akali ndi moyo; ndidzamuka ndikamuone iye ndisanafe.