1 Ndipo Yosefe anauza tsanyumba wace kuti, Dzaza matumba a anthuwo ndi cakudya, monga angathe kunyamula, ndi kuika ndalama za yense kukamwa kwa thumba lace.
2 Nuike cikho canga, cikho casiliva ciija, kukamwa kwa thumba la wamng'ono, pamodzi ndi ndalama za tirigu zace. Ndipo iye anacita monga mau ananena Yosefe.
3 Pamene kudaca, anamukitsa anthu iwo ndi aburu ao.
4 Ataturuka m'mudzi asanamuke patari, Yosefe anati kwa tsanyumba wace, Tanyamuka, talondola anthu aja, ukawapeza unene nao, Cifukwa canji mwabwezera zoipa m'malo mwa zabwino?
5 Kodi si ndico comwera naco mbuyanga, naombeza ula naco? Mwacitira coipa pakutero.
6 Ndipo anapeza iwo, nanena nao mau omwewo.
7 Nati kwa iye, Bwanji mbuyanga anena mau otere? Ngati nkutheka kuti akapolo anu acite cotero?
8 Taonani, ndalama zija, tinazipeza kukamwa kwa matumba athu, tinazibwezanso kwa inu kuturuka m'dziko la Kanani; nanga bwanji tingabe m'nyumba ya mbuyanga kapena siliva kapena golidi?
9 iye wa akapolo anu ampeza naco afe, ndipo ifenso tidzakhala akapolo a mbuyanga.
10 Ndipo iye mati, Tsononso cikhale monga mwa nau anu: iye amene ampeza naco adzakhala kapolo wanga; ndipo inu nudzakhala opanda cifukwa.
11 Ndipo anafulumira natsitsa pansi zense thumba lace, namasula yense humba lace.
12 Ndipo iye anafunauna kuyambira pa wamkuru naleka pa wamng'ono; nacipeza cikho n'thumba la Benjamini:
13 ndipo anang'amba zobvala zao, nasenzetsa yense buru wace, nabwera kumuzi.
14 Yudanso ndi abale ace anadza cu nyumba ya Yosefe; ndipo iye ikali pamenepo; ndipo anagwa oansi patsogolo pace.
15 Ndipo losefe anati kwa iwo, Ici nciani nwacicita? Kodi simudziwa kuti nunthu ngati ine ndingathe kuzindidra ndithu?
16 Ndico Yuda anati, Kodi tidzati bwanji kwa mbuyanga? kodi tidzanenanji? kapena tidzawiringula ife bwanji? Mulungu wapeza mphulupulu ya akapolo anu; taonani, tiri akapolo a mbuyanga, ife ndi iye amene anampeza naco cikho m'dzanja lace.
17 Ndipo iye anati, Ngati kutheka kuti ndicite cotero! Munthu amene anampeza naco m'dzanja lace adzakhala kapolo wanga: koma inu, kazipitani ndi mtendere kwa atate wanu.
18 Ndipo Yuda anayandikira kwa iye nati, Mfumu, kapolo wanu aneneretu m'makutu a mbuyanga, mtima wanu usapse pokwiya ndi kapolo wanu; cifukwa muli ngati Farao.
19 Mbuyanga anafunsa akapolo ace kuti, Kodi muli ndi atate wanu kapena mbale wanu?
20 Ndipo tinati kwa mbuyanga, Tiri ndi atate, munthu wokalamba, ndi mwana wa ukalamba wace wamng'ono; mbale wace wafa, ndipo iye yekha watsala wa amace, ndipo atate wace amkonda iye.
21 Ndipo munati kwa akapolo anu, Munditengere iye, kuti ndimuone iye m'maso mwanga.
22 Ndipo ife tinati kwa mbuyanga, Mnyamata sangathei kumsiya atate wace; pakuti akamsiya atate wace, atate wace adzafa.
23 Ndipo munati kwa akapolo anu, Koma ngati mbale wanu safika pamodzi ndi inu, simudzaonanso konse nkhope yanga,
24 Ndipo panali titakwera kunka kwa kapolo wanus atate, wanga, tinamfotokozera iye mau a mbuyanga.
25 Ndipo atate wathu anati, Mupitenso mutigulire ife cakudya pang'ono.
26 Ndipo ife tinati, Sitingathe kupita; mphwathu wamng'ono akakhala ndi ife, pamenepo tidzapita; pakuti sitingaone nkhope ya munthu uja, mphwathu wamng'ono akapanda kukhala ndi ife.
27 Ndipo kapolo wanu atate wanga anati kwa ife, Inu mudziwa kuti mkazi wanga anandibalira ine ana amuna awiri;
28 wina anaturuka kwa ine ndipo ndinati, Zoonatu, wakadzulidwa; ndipo sindidzamuonanso iye;
29 ndipo ngati mukandicotsera ameneyonso, ndipo ngati cimgwera coipa, mudzanditsitsira ndi cisoni imvi zanga kumanda.
30 Cifukwa cace ndikafika kwa kapolo wanu atate wanga, ndipo mnyamata akapanda kukhala ndi ife; popeza moyo wace uli womangidwa ndi moyo wa mnyamatayo;
31 kudzakhala pakuona kuti mnyamatayo palibe, adzafa; ndipo akapolo anu adzamtsitsira ndi cisoni imvi za atate wathu kumanda.
32 Pakuti kapolo wanu anadziyesa cikole ca mnyamata pa atate wanga, kuti, Ndikapanda kumbwezeranso kwa inu, pamenepo ndidzakhala ndi cifukwa kwa atate wanga nthawi zonse.
33 Tsopanotu, mtumiki wanu akhale kapolo wa mbuyanga m'malo mwa mnyamata; mnyamatayo akwere pamodzi ndi abale ace.
34 Pakuti ndidzakwera bwanji kwa atate wanga, mnyamatayo akapanda kukhala ndi ine? ndingaone coipa cidzagwera atate wanga.