Genesis 24 BL92

Rebeka apalidwa ubwenzi ndi Isake

1 Ndipo Abrahamu anali wokalamba, nagonera zaka zambiri; ndipo Yehova anadalitsa Abrahamu m'zinthu zonse.

2 Ndipo Abrahamu anati kwa mnyamata wace wamkuru wa pa nyumba yace, amene analamulira pa zonse anali nazo, Taikatu dzanja lako pansi pa ncafu yanga:

3 ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana akazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.

4 Koma udzanke ku dziko langa, kwa abale anga, ndi kumtengera mwana wanga Isake mkazi.

5 Ndipo anati kwa iye mnyamatayo, Kapena sadzafuna mkaziyo kunditsata ine ku dziko lino: kodi ndikambwezerenso mwana wanu kudziko komwe mwacokera inu?

6 Ndipo Abrahamu anati kwa iye, Cenjera iwe, usambwezerenso mwana wanga kumeneko.

7 Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene ananditenga ine ku nyumba ya atate wanga, ku dziko la abale anga, amene ananena ndi ine, amene analumbirira ine kuti, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili; iye adzatumiza mthenga wace akutsogolere, ndipo udzamtengere mwana wanga mkazi kumeneko.

8 Ndipo ngati sadzafuna mkaziyo kukutsata iwe, udzakhala wosacimwa pa cilumbiro cangaci: koma mwana wanga usambwezerenso kumeneko.

9 Ndipo mnyamatayo anaika dzanja lace pansi pa ncafu yace ya Abrahamu mbuye wace, namlumbirira iye za cinthuco.

10 Ndipo mnyamatayo anatenga ngamila khumi za mbuyace, namuka: cifukwa kuti cuma conse ca mbuyace cinali m'dzanja lace: ndipo anacoka namuka ku Mesopotamiya, ku mudzi wa Nahori.

11 Ndipo anagwaditsa ngamila zace kunja kwa mudzi, ku citsime ca madzi nthawi yamadzulo, nthawi yoturuka akazi kudzatunga madzi.

12 Ndipo anati, Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu mundiyendetse ine bwino lero lino, mumcitire ufulu mbuyanga Abrahamu,

13 Taonani, ine ndiima pa citsime ca madzi; ndipo ana akazi a m'mudzi aturuka kudzatunga madzi;

14 ndipo pakhale kuti namwali amene ndidzati kwa iye, Tulatu mtsuko wako, ndimwe; ndipo iye adzati, Imwa, ndipo ndidzamwetsanso ngamila zako; yemweyo akhale mkazi wosankhira mnyamata wanu Isake; ndipo cotero ndidzadziwa kuti mwamcitira mbuyanga ufulu.

15 Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anaturuka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwace wa Abrahamu, ndi mtsuko wace paphewa pace.

16 Ndipo namwaliyo anali wokongola kwambiri m'maonekedwe ace, ndiye namwali wosamdziwa mwamuna, ndipo anatsikira kukasupe, nadzaza mtsuko wace, nakwera.

17 Ndipo mnyamatayo anamthamangira kukomana naye, nati, Ndimwetu madzi pang'ono a m'mtsuko mwako.

18 Ndipo anati, Imwa mbuyanga; nafulumira nayangata mtsuko m'manja mwace namwetsa iye.

19 Atatha kumwetsa iye, anati, Ndidzatungiranso ngamila zako, mpaka zitamwa zonse.

20 Ndipo anafulumira nathira madzi a m'mtsuko wace m'comwera, nathamangiranso kucitsime kukatunga, nazitungira ngamila zace zonse.

21 Munthuyo ndipo anamyang'anira iye, nakhala cete, kuti adziwe ngati Yehova anamuyendetsa bwino kapena iai.

22 Ndipo panali zitatha kumwa ngamila, munthuyo anatenga mphete yagolidi ya kulemera kwace sekele latheka, ndi zingwinjiri ziwiri za m'manja ace, kulemera kwace masekele khumi a golidi.

23 Ndipo anati, Ndiwe mwana wa yani? Undiuzetu. Kodi ku nyumba ya atate wako kuli malo akuti tigoneko ife?

24 Ndipo mkaziyo anati kwa iye, Ine ndine mwana wa Betuele mwana wamwamuna wa Milika, amene anambalira Nahori.

25 Natinso kwa iye, Tiri nao maudzu ndi zakudya zambiri oeli malo ogona.

26 Munthuyo oelipo anawerama mutu namyamika Yehova.

27 Ndipo anati, Ayamikike Yehova Mulungu wa mbuyanga Abrahamuamene sanasiya mbuyanga wopanda cifundo cace ndi zoona zace: koma ine Yehova Wanditsogolera m'njira ya ku nyumba ya abale ace a mbuyanga.

28 Namwaliyo ndipo anathamanga nawauza zimenezo ku nyumba ya amace.

29 Ndipo Rebeka anali ndi mlongo wace dzina lace Labani; ndipo Labani anathamangira munthuyo kunja ku kasupe.

30 Ndipo panali, pamene anaona mphete ndi zingwinjiri pa manja a mlongo wace, pamene anamva mau a Rebeka mlongo wace, akuti, Cotero ananena ndi ine munthuyo; Labani anafika pa munthuyo; taonani, anaimirira pa ngamila pakasupe.

31 Ndipo anati, Talowa iwe, wodalitsidwa ndi Yehova; uimiriranji kunjako? cifukwa kuti ndakonzeratu nyumba, ndi malo a ngamila.

32 Munthuyo ndipo analowa m'nyumba, namasula ngamila, napatsa ngamila maudzu ndi cakudya, ndi madzi akusamba mapazi ace ndi mapazi a iwo amene anali naye.

33 Ndipo anaika cakudya pamaso pace: koma anati, Sindidzadya ndisananene cimene ndadzera. Ndipo anati, Nenatu.

34 Ndipo anati, Ine ndine mnyamata wa Abrahamu.

35 Yehova wamdalitsa mbuyanga kwambiri; ndipo anakula kwakukuru; ndipo anampatsa iye nkhosa ndi ng'ombe, ndi siliva ndi golidi, ndi akapolo ndi adzakazi, oeli ngamila ndi aburu.

36 Ndipo Sara mkazi wace wa mbuyanga anambalira mbuyanga mwana wamwamuna, mkaziyo anali wokalamba; ndipo anampatsa mwanayo zonse ali nazo.

37 Ndipo mbuyanga anandilumbiritsa ine kuti, Usamteogere mwana wanga mkazi wa ana akazi a Kanani, m'dziko mwao m'mene ndikhala ine;

38 koma udzanke ku nyumba ya atate wanga, kwa abale anga, ndi kumtengera mwana wanga mkazi.

39 Ndipo ndinati kwa mbuyanga, Kapena mkazi sadzanelitsata ine.

40 Ndipo anati kwa ine, Yehova, amene ndiyenda ine pamaso pace, adzatumiza mthenga wace pamodzi ndi iwe, nadzakuyendetsa bwino m'njira yako; ndipo ukamteogere mwana wanga mkazi wa mwa abale anga ndi ku nyumba ya atate wanga;

41 ukatero udzakhala wosacimwa pa malumbiro ako, pofika iwe kwa abate anga; ndipo ngati sadzakupatsa iwe, udzakhala wosacimwa pa malumbiro ako.

42 Ndipo ndinafika lero kukasupe, ndipo ndinati, Yehova Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, ngati mundiyendetsatu bwino njira yanga m'mene ndinkamo ine;

43 taonani, ine ndiima pa kasupe wa madzi, ndipo pakhale, kuti namwali amene aturuka kudzatunga madzi, ndikati kwa iye, Ndipatse madzi ndimwe pang'ono m'mtsuko mwako;

44 ndipo iye akati kwa ine, Imwatu iwe, ndiponso ndidzatungira ngamila zako; yemweyo akhale mkazi amene Yehova wamsankhira mwana wa mbuyanga.

45 Ndisanathe kunena m'mtima mwanga, taonani, Rebeka anaturuka ndi mtsuko wace pa phewa lace, natsikira kukasupe, natunga: ndipo ndinati kwa iye, Ndimwetu.

46 Ndipo iye anafulumira, natsitsa mtsuko pa phewa lace, nati, Imwatu, ndipo ndidzamwetsanso ngamila zako: ndipo ndinamwa, ndipo anamwetsa ngamila.

47 Ndipo ndinamfunsa iye kuti, Ndiwe mwana wa yani kodi? Ndipo anati, Ndine mwana wa Betuele, mwana wa Nahori amene anambalira iye Milika: ndipo ndinaika mphete pamphuno pace ndi zingwinjiri pa manja ace.

48 Ndipo ndinawerama mutu wanga ndi kulambira Yehova, ndi kumyamikira Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, amene ananditsogolera ine m'njira yakuona, kuti ndikamtengere mwana wamwamuna wace mwana wamkazi wa mphwace wa mbuyanga.

49 Tsopano, ngati mudzamcitira mbuyanga zaufulu ndi zoonadi, mundiuze, ngati iai, mundiuze; kuti ndipatukire ku dzanja lamanja kapena ku dzanja lamanzere.

50 Ndipo anayankha Labani ndi Betuele, nati, Caturuka kwa Yehova cinthu ici; sitingathe kunena ndi iwe coipa kapena cabwino.

51 Taonani, Rebeka ali pamaso pako, mtenge ndi kumuka, akhale mkazi wa mwana wa mbuyako, monga wanena Yehova.

52 Ndipo panali pamene anamva mauwo mnyamata wa Abrahamu, anamgwadira Yehova pansi,

53 Ndipo mnyamatayo anaturutsa zokometsera zasiliva ndi zokometsera zagolidi, ndi zobvala, nampatsa Rebeka: ndipo anapatsa za mtengo wapatari kwa mlongo wace ndi amace.

54 Ndipo anadya namwa iye ndi anthu amene anali pamodzi naye, nagonapo usiku: ndipo anauka m'mamawa, ndipo iye anati, Mundilole ine ndinke kwa mbuyanga.

55 Ndipo mlongo wace ndi amace anati, Namwali akhale ndi ife masiku akuwerengeka, afikire khumi; patsogolo pace iye adzamuka.

56 Ndipo iye anati kwa iwo, Musandicedwetse ine, pakuti Yehova wandiyendetsa bwino m'njira yanga: mundilole ine ndinke kwa mbuyanga.

57 Ndipo anati iwo, Tidzamuitana namwaliyo, tidzamfunsa pakamwa pace.

58 Ndipo anamuitana Rebeka nati kwa iye, Kodi udzanka pamodzi ndi munthuyo? Ndipo anati, Ndidzanka.

59 Ndipo anamlola Rebeka mlongo wao ndi mlezi wace, amuke pamodzi ndi mnyamata wace wa Abrahamu, ndi anthu ace.

60 Ndipo anamdalitsa Rebeka, nati kwa iye, Mlongo wathu ndiwe, iwe ukhale amai wa anthu zikwizikwi, mbeu zako zigonjetse cipata ca iwo akudana nao.

61 Ndipo adauka Rebeka ndi anamwali ace, nakwera pa ngamila natsata munthuyo: mnyamatayo ndipo anamtenga Rebeka namuka.

62 Ndipo Isake anadzera njira ya Beereahai-roi; cifukwa kuti anakhala iye n'dziko la kumwera.

63 Ndipo Isake anaturuka kulingalira m'munda madzulo; ndipo anatukula maso ace, nayang'ana, taona, ngamila zinalinkudza,

64 Ndipo Rebeka anatukula maso ace, ndipo pamene anaonalsake anatsika pa ngamila,

65 Ndipo anati kwa mnyamata, Munthuyo ndani amene ayenda m'munda kukomana ndi ife? Mnyamatayo ndipo anati, Uyo ndi mbuyanga: cifukwa cace namwali anatenga cophimba cace nadziphimba.

66 Mnyamatayo ndipo anamuuza Isake zonse anazicita.

67 Ndipo Isake anamlowetsa mkaziyo m'hema wa amace Sara, namtenga Rebeka, nakhala iye mkazi wace; ndipo anamkonda iye; ndipo Isake anatonthozedwa mtima atafa amace.