Genesis 38 BL92

Yuda ndi Tamara

1 Ndipo panali nthawi yomweyo, kuti Yuda anatsikira kwa abale ace nalowa kwa M-adulami, dzina lace Hira.

2 Ndipo Yuda anaona kumeneko mwana wamkazi wa Mkanani dzina lace Sua: ndipo anamtenga, nalowa kwa iye.

3 Ndipo anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namucha dzina lace Eri.

4 Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna, namucha dzina lace Onani.

5 Ndipo anabalanso mwana wamwamuna, namucha dzina lace Sela: ndipo iye anali pa Kezibi pamene mkazi anambala iye,

6 Ndipo Yuda anamtengera Eri mwana wace woyamba mkazi, ndipo dzina lace ndilo Tamara.

7 Koma Eri mwana wace woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova: ndipo Yehova anamupha iye.

8 Ndipo Yuda anati kwa Onani, Lowani naye mkazi wa mbale wako, ndi kumcitira mkazi zoyenera mphwace wa mwamuna wace, ndi kumuukitsira mkuru wako mbeu.

9 Ndipo Onani anadziwa kuti mbeu siidzakhala yace: ndipo panali pamene iye analowana naye mkazi wa mbale wace, kuti anaitaya pansi, kuti angampatse mbeu kwa mkuru wace.

10 Koma cimene iye anacita cinali coipa pamaso pa Mulungu, ndipo anamupha iyenso.

11 Ndipo Yuda anati kwa Tamara mpengozi wace, Khala wamasiye m'nyumba ya atate wako, kufikira akakula msinkhu Sela mwana wanga wamwamuna; cifukwa anati kuti, Angafe iyenso monga abale ace. Ndipo Tamara ananka nakhala m'nyumba ya atate wace.

12 Atacuruka masiku mwana wamkazi wa Sua, mkazi wace wa Yuda anafa; ndipo Yuda anatonthola mtima, nakwera kunka kwa akusenga nkhosa zace ku Timna, iye ndi bwenzi lace Hira, M-adulami.

13 Ndipo anamuuza Tamara, kuti, Taona, mpongozi wako akwera kunka ku Timna kuti akasenge nkhosa zace.

14 Pamenepo anabvula zobvala zacezamasiye, nadzipfundandi copfunda cace, nabvala nakhala pa cipata ca Enaimu, cifukwa ciri pa njira ya ku Timna; pakuti anaona kuti Sela anakula msinkhu, ndipo sanampatsa iye kuti akhale mkazi wace.

15 Pamene Yuda anamuona iye, anaganizira kuti ali mkazi wadama: cifukwa iye anabisa nkhope yace.

16 Ndipo iye anapatukira kwa mkazi panjira, nati, Tiyetu, ndilowane nawe; cifukwa sanamdziwa kuti ndiye mpongozi wace. Ndipo anati, Kodi udzandipatsa ine ciani kuti ulowane ndi ine.

17 Ndipo iye anati, Ndidzatumiza kwa iwe kamwana ka mbuzi ka m'ziweto. Ndipo mkazi nati, Kodi udzandipatsa ine cikole mpaka ukatumiza?

18 Ndipo iye anati, Cikole canji ndidzakupatsa iwe? Ndipo mkazi anati, Mphete yako, ndi cingwe cako, ndi ndodo iri m'dzanja lako. Ndipo anampatsa izo, nalowana naye, ndipo mkazi anatenga pakati ndi iye.

19 Ndipo mkazi anauka nacoka, nabvula copfunda cace, nabvala zobvala zamasiye zace.

20 Ndipo Yuda anatumiza kamwana ka mbuzi ndi dzanja la bwenzi lace Madulami, kuti alandire cikole pa dzanja la mkazi; koma sanampeza iye.

21 Ndipo anafunsa amuna a pamenepo kuti, Ali kuti wadama uja anali pambali pa njira pa Enaimu? ndipo iwo anati, Panalibe wadama pano.

22 Ndipo iye anabwera kwa Yuda nati, Sitinampeza mkazi; ndiponso amuna a pamenepo anati, Panalibe wadama pano.

23 Ndipo Yuda anati, Azilandire kuti tingacitidwe manyazi: taona, ndinatumiza mwana uyu wa mbuzi, ndipo sunampeza iye.

24 Ndipo panali itapita miyezi itatu, anamuuza Yuda kuti, Tamara mpongozi wako wacita cigololo, ndiponso taonani, ali ndi pakati ndi cigololoco. Ndipo Yuda anati, Mturutse iye kuti amponye pamoto.

25 Pamene anamturutsa Iye, mkazi anatumiza kwa mpongozi wace kuti, Ndi mwamuna mwini izi ndatenga pakati; ndipo mkazi anati, Tayang'anatu, za yani zimenezi, mphete, ndi cingwe, ndi ndodo?

26 Ndipo Yuda anabvomereza nati, Akhale wolungama wopambana ine, cifukwa ine sindinampatsa iye Sela mwana wanga wamwamuna. Ndipo iye sanamdziwanso mkaziyo.

27 Ndipo panali nthawi ya kubala kwace, taonani, amapasa anali m'mimba mwace.

28 Ndipo panali pamene anabala kuti mmodzi anaturutsa dzanja; ndipo namwino anatenga cingwe cofiira namanga pa dzanja lace, kuti, Uyu anayamba kubadwa.

29 Ndipo panali pamene iye ana bweza dzanja lace, kuti, taona, mbale wace anabadwa, ndipo namwino anati, Wadziposolera wekha bwanji? cifukwa cace dzina lace linachedwa Pereze.

30 Ndipo pambuyo pace anabadwa mbale wace, amene anali ndi cingwe cofiira pamkono pace, dzina lace linachedwa Zera.