Genesis 21 BL92

Kubadwa kwa Isake

1 Ndipo Yehova anayang'anira Sara monga momwe anati, ndipo Yehova anamcitira iye monga ananena.

2 Ndipo Sara anatenga pakati, nambalira Abrahamu m'ukalamba wace mwana wamwamuna, nthawi yomweyo Mulungu anamuuza iye.

3 Ndipo Abrahamu anamucha dzina lace la mwana wace wamwamuna amene anabala iye, amene anambalira iye Sara, Isake.

4 Ndipo Abrahamu anamdula mwana wace wamwamuna Isake pamene anali wa masiku ace asanu ndi atatu, monga Mulungu anamlamulira iye.

5 Ndipo Abrahamu anali wa zaka zana limodzi pamene anambadwira iye Isake mwana wace.

6 Ndipo Sara anati, Mulungu anandisekeretsa ine; onse akumva adzasekera pamodzi ndi ine.

7 Ndipo anati, Akadatero ndani kwa Abrahamu kuti Sara adzayamwitsa ana? pakuti ndambalira iye mwana wamwamuna m'ukalamba wace.

Abrahamu acotsa Hagara

8 Ndipo anakula mwanayo naletsedwa kuyamwa: ndipo Abrahamu anakonza madyerero akuru tsiku lomwe analetsedwa Isake kuyamwa.

9 Ndipo Sara anaona mwana wace wamwamuna wa Hagara M-aigupto, amene anambalira Abrahamu, alinkuseka.

10 Cifukwa cace anati kwa Abrahamu, Cotsa mdzakazi uyo, ndi mwana wace wamwamuna; cifukwa mwana wa mdzakazi uyo sadzalowa m'nyumba pamodzi naye mwana wanga Isake.

11 Ndipo mauwo anaipira Abrahamu cifukwa ca mwana wace.

12 Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Usaipidwe nao, cifukwa ca mnyamatayo, ndi cifukwa ca mdzakazi wako; momwe monse akunenera iwe Sara umvere iwe mau ace; cifukwa kuti mwa Isake zidzaitanidwa mbeu zako.

13 Ndipo mwana wamwamuna wa mdzakazi uyo ndidzayesa mtundu, cifukwa iye ndiye mbeu yako.

14 Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi mcenje wa madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pace, ndi mwana, namcotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocerera m'cipululu ca Beereseba.

15 Ndipo anatha madzi a m'mcenje ndipo anaika mwana pansi pa citsamba.

16 Ndipo ananka nakhala pansi popenyana naye patari, monga pakugwa mubvi: cifukwa anati, Ndisaone kufa kwa mwana. Ndipo anakhala popenyana naye, nakweza mau ace nalira,

17 Ndipo Mulungu anamva mau a mnyamatayo, ndi mthenga wa Mulungu anamuitana Hagara, ndi mau odzera kumwamba, nati kwa iye, Watani Hagara? usaope; cifukwa Mulungu anamva mau a mnyamata kumene ali.

18 Tauka, nuukitse mnyamatayo, ndi kumgwira m'dzanja lako; cifukwa ndidzamuyesa iye mtundu waukuru.

19 Ndipo Mulungu anamtsegula m'maso mwace, ndipo anaona citsime ca madzi; namuka nadzaza mcenje ndi madzi, nampatsa mnyamata kuti amwe.

20 Ndipo Mulungu anakhala ndi mnyamata, ndipo anakula iye; nakhala m'cipululu, nakhala wauta.

21 Ndipo anakhala m'cipululu ca Parana; ndipo amace anamtengera iye mkazi wa ku dziko la Aigupto.

Abrahamu apangana ndi Abimeleke

22 Ndipo panali nthawi yomweyo. Abimeleke ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yace anati kwa Abrahamu, kuti, Mulungu ali pamodzi ndi iwe m'zonse uzicita iwe;

23 tsopano iwe undilumbirire ine pano pa Mulungu kuti sudzandinyenga ine, kapena mwana wanga, kapena mdzukulu wanga: koma monga ufulu ndakucitira iwe udzandicitire ine, ndi dziko lomwe wakhalamo, ngati mlendo.

24 Ndipo Abrahamu anati, Ine ndidzalumbira.

25 Ndipo Abrahamu anamdzudzula Abimeleke cifukwa ca citsime ca madzi, anyamata ace a Abimeleke anacilanda.

26 Ndipo anati Abimeleke, Sindinadziwe amene anacita ico; ndipo iwe sunandiuze ine, ndiponso sindinamve koma lero lino.

27 Ndipo Abrahamu anatenga nkhosa ndi ng'ombe, nampatsa Abimeleke, ndipo anapangana pangano onse awiriwo.

28 Ndipo Abrahamu anapatula ana a nkhosa akazi asanu ndi awiri pa okha.

29 Ndipo Abimeleke anati kwa Abrahamu, Nanga ana a nkhosa akazi asanu ndi awiri amene wapatula pa okha?

30 Ndipo anati, Ana a nkhosa akazi asanu ndi awiriwa uwalandire pa dzanja langa, kuti akhale mboni zanga, kuti ndakumba ine citsime cimeneci.

31 Cifukwa cace anacha malowo Beereseba: cifukwa pamenepo analumbira onse awiri.

32 Ndipo anapangana pangano pa Beereseba: ndipo anauka Abimeleke ndi Fikolo kazembe wa-nkhondo yace, nabwera kunka ku dziko la Afilisti.

33 Ndipo Abrahamu ananka mtengo wabwemba pa Beereseba, naitanira pamenepo dzina la Yehova, Mulungu wa nthawi zonse.

34 Ndipo Abrahamu anakhala ngati mlendo masiku ambiri m'dziko la Afilisti.