Genesis 23 BL92

Imfa ndi kuikidwa kwa Sara

1 Ndipo Sara anali wa zaka zana limodzi kudza makumi awiri ndi zisanu ndi ziwiri: ndizo zaka za moyo wa Sara.

2 Ndipo Sara anafa m'Kiriyati-araba (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani; ndipo Abrahamu anadza ku maliro a Sara, kuti amlire.

3 Ndipo Abrahamu anauka pa wakufa wace, nanena kwa ana a Heti, nati,

4 Ine ndine mlendo wakukhala ndi inu: mundipatse ndikhale ndi manda pamodzi ndi inu, kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso.

5 Ndipo ana a Heti anayankha Abrahamu nati kwa iye,

6 Mutimvere ife mfumu, ndinu karonga wamkuru pakati pa ife; muike wakufa wanu m'manda mwathu mosankhika: palibe munthu yense wa ife adzakaniza manda ace, kuti muike wakufa wanu.

7 Ndipo anauka Abrahamu naweramira anthu a m'dzikomo, ana a Heti.

8 Ndipo ananena nao, kuti, Ngati mukandibvomereza kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso, mundimvere ine, mundinenere ine kwa Efroni mwana wace wa Zohari,

9 kuti andipatse ine phanga la Makipela, limene liri pansonga pa munda wace; pa mtengo wace wonse andipatse pakati pa inu, ndikhale nao manda.

10 Ndipo Efroni anakhala pakati pa ana a Heti: ndipo Efroni Mhiti anayankha Abrahamu alinkumva ana a Heti, onse amene analowa pa cipata ca mudzi wace, kuti,

11 Iai, mfumu, mundimvere ine; munda ndikupatsani inu, ndi phanga liri m'menemo ndikupatsani inu, pamaso pa ana a anthu anga ndikupatsani inu; ikani wakufa wanu.

12 Ndipo Abrahamu anawerama pamaso pa anthu a m'dzikomo.

13 Ndipo ananena kwa Efroni alinkumva anthu a m'dzikomo, kuti, Koma ngati ufuna, undimveretu ine: ndidzakupatsa iwe mtengo wace wa munda; uulandire kwa ine, ndipo ndidzaika wakufa wanga m'menemo.

14 Ndipo Efroni anamyankha Abrahamu, nati kwa iye,

15 Mfumu, mundimvere ine; kadziko ka mtengo wace wa masekele a siliva mazana anai, ndiko ciani pakati pa ine ndi inu? ikani wakufa wanu.

16 Ndipo Abrahamu anamvera Effoni, ndipo Abrahamu anamuyesera Efroni ndalama zimene ananena alinkumva ana a Heti, masekele a siliva mazana anai, ndalama zomwezo agulana nazo malonda.

17 Ndipo munda wa Efroni umene unali m'Makipela, umene unali patsogolo pa Mamre, munda ndi phanga liri momwemo, ndi mitengo yonse inali m'mundamo, yokhala m'malire monse mozungulira momwemo,

18 inalimbitsidwa kwa Abrahamu ikhale yace, pamaso pa ana a Heti, pa onse amene analowa pa cipata ca mudzi wace.

19 Zitatha izi Abrahamu anaika Sara mkazi wace m'phanga la munda wa Makipela patsogolo pa Mamre (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani.

20 Ndipo ana a Heti analimbitsira Abrahamu munda, ndi phanga liri m'menemo, likhale lace lamanda.