1 Ndipo Israyeli anamuka ulendo wace ndi zonse anali nazo, nafika ku Beereseba, napereka nsembe kwa Mulungu wa Isake atate wace.
2 Ndipo Mulungu ananena kwa Israyeli, m'masomphenya a usiku, nati, Yakobo, Yakobo.
3 Nati iye, Ndine pano. Ndipo anati, Ine ndine Mulungu, Mulungu wa atate wako; usaope kunka ku Aigupto; pakuti pamenepo ndidzakusandutsa iwe mtundu waukuru;
4 Ine ndidzatsikira pamodzi ndi iwe ku Aigupto; ndipo Ine ndidzakubwezanso ndithu; ndipo Yosefe adzaika dzanja lace pamaso pako.
5 Ndipo Yakobo anacoka ku Beereseba, ndipo ana amuna a Israyeli anamnyamula Yakobo atate wao, ndi ana ao ang'ono, ndi akazi ao, m'magareta amene Farao anatumiza kuti amnyamule iye,
6 Ndipo anatenga ng'ombe zao ndi cuma cao anacipezam'dziko la Kanani, nadza ku Aigupto, Yakobo ndi mbeu zace zonse pamodzi ndi iye;
7 ana ace amuna, ndi zidzukulu zace zazimuna, ndi ana akazi ace, ndi zidzukulu zace zazikazi, ndi mbeu zace zonse anadza nazo m'Aigupto.
8 Maina a ana a Israyeli amene anadza m'Aigupto ndi awa: Yakobo ndi ana amuna ace: Rubeni mwana wamwamuna woyamba wa Yakobo.
9 Ndi ana amuna a Ruberu Hanoki, ndi Palu, ndi Hezroni, ndi Karmi.
10 Ndi ana amuna a Simeoni: Yemueli ndi Yamini, ndi Ohadi, ndi Yakini, ndi Zohari, ndi Sauli, mwana wamwamuna wa mkazi wa ku Kanani.
11 Ndi ana amuna a Levi: Gerisoni, Kohati, ndi Merai.
12 Ndi ana amuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana amuna a Perezi ndiwo Hezroni ndi Hamuli.
13 Ndi ana amuna a Isakara: Tola ndi Puva, ndi Yabi, ndi Simroni.
14 Ndi ana amuna a Zebuloni: Seredi, ndi Eloni ndi Yaledi.
15 Amenewo ndi ana amuna a Leya, amene anambalira Yakobo m'Padanaramu, pamodzi ndi mwana wamkazi wace Dina; ana amuna ndi akazi onse: ndiwo anthu makumi atatu kudza atatu.
16 Ndi ana amuna a Gadi: Zifioni, ndi Hagi, ndi Suni, ndi Ezboni, ndi Eri, ndi Arodi, ndi Areli.
17 Ndi ana amuna a Aseri: Yimna, ndi Yisiva, ndi Yisivi, ndi Beriya, ndi Sera mlongo wao; ndi ana a Beriya: Hebere, ndi Maliki eli.
18 Amenewa ndi ana a Zilipa, amene Labani anampatsa Leya mwana wace wamkazi, amenewo anambalira Yakobo, anthu khumi ndi asanu ndi mmodzi.
19 Ana a Rakele mkazi wace wa Yakobo: Yosefe ndi Benjamini.
20 Kwa Yosefe kunabadwa m'dziko la Aigupto Manase ndi Efraimu, amene Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni anambalira iye.
21 Ndi ana amuna a Benjamini: Bela ndi Bekeri, ndi Asibeli, ndi Gera, ndi Namani, ndi Ehi ndi Rosi, Mupimu ndi Hupimu, ndi Aridi.
22 Amenewo ndi ana a Rakele, amene anabadwira Yakobo; anthu onse ndiwo khumi ndi anai.
23 Ndi ana amuna a Dani: Husimu.
24 Ndi ana amuna a Nafitali: Yazeeli, ndi Guni, ndi Yezera ndi Silemu.
25 Amenewa ndi ana a Biliha, amene Labani anampatsa Rakele mwana wace wamkazi, amenewo anambalira Yakobo; anthu onse ndiwo asanu ndi awiri.
26 Ndi anthu onse amene anadza ndi Yakobo m'Aigupto, amene anaturuka m'cuuno mwace, pamodzi ndi akazi a ana amuna a Yakobo ndiwo makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi mmodzi;
27 ndi ana amuna a Yosefe, amene anambadwira iye m'Aigupto ndiwo anthu awiri; anthu onse a mbumba ya Yakobo, amene analowa m'Aigupto anali makumi asanu ndi awiri.
28 Ndipo anatumiza Yuda patsogolo pace kwa Yosefe, amtsogolere kumuonetsa njira yomka ku Goseni: ndipo anafika ku dziko la Goseni.
29 Ndipo Yosefe anamanga gareta lace nakwera kunka kukakomana naye Israyeli atate wace, ku Goseni, ndipo anadzionetsera yekha kwa iye, nagwera pakhosi pace nakhala m'kulira pakhosi pace.
30 Ndipo Israyeli anati kwa Yosefe, Ndife tsopano, popeza ndaona nkhope yako, kuti ukali ndi moyo.
31 Ndipo Yosefe anati kwa abale ace, ndi kwa mbumba ya atate wace, Ndidzanka, ndikauze Farao, ndipo ndidzati kwa iye, Abale anga ndi mbumba ya atate wanga, amene anali m'dziko la Kanani, afika kwa ine;
32 ndipo anthuwo ali abusa cifukwa anakhala oweta ng'ombe; ndipo anadza ndi nkhosa zao ndi ng'ombe zao ndi zonse ali nazo.
33 Ndipo padzakhala pamene Farao adzaitana inu, nadzati, Nchito yanu njotani?
34 mudzati, Akapolo anu akhala oweta ng'ombe ciyambire ubwana wathu kufikira tsopano, ife ndi atate athu; kuti mukhale m'dziko la Goseni; a cifukwa abusa onse anyansira Aaigupto.