Genesis 16 BL92

Sara ndi Hagara

1 Ndipo Sarai mkazi wace wa Abramu sanambalire iye mwana; ndipo anali ndi mdzakazi, wa ku Aigupto, dzina lace Hagara.

2 Ndipo Sarai anati kwa Abramu, Taonanitu, Yehova anandiletsa ine kuti ndisabale: lowanitu kwa mdzakazi wanga; kapena ndikalandire ndi iye ana. Ndipo Abramu anamvera mau a Sarai.

3 Ndipo Sarai mkazi wace wa Abramu anatenga Hagara mdzakazi wace wa ku Aigupto, Abramu atakhala m'dziko la Kanani zaka khumi, nampereka iye kwa Abramu mwamuna wace, kuti akhale mkazi wace.

4 Ndipo analowa kwa Hagara, ndipo iye anatenga pakati. Pamene anaona kuti anatenga pakati, anapeputsa wakuka wace m'maso mwace.

5 Ndipo Sarai anati kwa Abramu, Kusauka kwanga kukhale pa iwe: ndakupatsa iwe mdzakazi wanga pamtima pako; ndipo pakuona kuti anatenga pakati anandipeputsa ine m'maso mwace: Yehova aweruze pakati pa iwe ndi ine.

6 Koma Abramu anati kwa Sarai, Taona, mdzakazi wako ali m'dzanja lako, umcitire iye cimene cikukomera m'maso mwako. Ndipo Sarai anamsautsa iye, ndipo anathawa kumaso kwace.

7 Ndipo mthenga wa Yehova anampeza iye pa kasupe wa madzi m'cipululu, pa kasupe wa pa njira ya ku Suri.

8 Ndipo anati, Hagara, mdzakazi wace wa Sarai, ufumira kuti? Unka kuti? Ndipo anati, Ndithawa ine kumaso kwace kwa wakuka wanga Sarai.

9 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Bwera kwa wakuka wako, udzicepetse wekha pamanja pace.

10 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Ndidzacurukitsa ndithu mbeu zako, kuti unyinji wao sudzawerengeka.

Kubadwa kwa Ismayeli

11 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Taona, uli ndi pakati, ndipo udzabala mwana wamwamuna; nudzamucha dzina lace Ismayeli; cifukwa Yehova anamva kusauka kwako.

12 Ndipo iye adzakhala munthu wa m'thengo; ndipo dzanja lace lidzakhala lotsutsana ndi anthu onse, ndi manja a anthu onse adzakhala otsutsana naye: ndipo iye adzakhala pamaso pa abale ace onse.

13 Ndipo anacha dzina la Yehova amene ananena naye, Ndinu Mulungu wakundiona ine; pakuti anati, Kodi kunonso ndayang'ana pambuyo pace pa iye amene wakundiona ine?

14 Cifukwa cace citsimeco cinachedwa Beerelahai-roi; taonani ciri pakati pa Kadese ndi Berede.

15 Ndipo Hagara anambalira Abramumwana wamwamuna, ndipo Abramu anacha dzina la mwana wace amene anambalira iye Hagara, lsmayeli.

16 Ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi atatu kudza zisanu ndi cimodzi, pamene Hagara anambalira Abramu Ismayeli.