6 Ndipo Abramu anapitira m'dziko kufikira ku malo a Sekemu, kufikira ku mtengo wathundu wa ku More. Akanani anali m'dzikomo nthawi yomweyo.
7 Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye.
8 Ndipo iye anacoka kumeneko kunka ku phiri la kum'mawa kwa Beteli, namanga hema wace; Beteli anali kumadzulo, ndi Ai anali kum'mawa: kumeneko ndipo anammangira Yehova guwa la nsembe, naitanira dzina la Yehova.
9 Ndipo Abramu anayenda ulendo wace, nayendayenda kunka kumwela.
10 Ndipo munali njala m'dzikomo, ndipo anatsikira Abramo ku Aigupto kukakhala kumeneko, cifukwa kuti njala inali yaikuru m'dziko m'menemo.
11 Ndipo panali pamene anayandikira kulowa m'Aigupto, anati kwa Sarai mkazi wace, Taonani, ndidziwa kuti ndiwe mkazi wokongola maonekedwe ako;
12 ndipo padzakhala pamene adzakuona iwe Aaigupto, adzati, Uyu ndi mkazi wace: ndipo adzandipha ine, koma iwe adzakuleka ndi moyo.