3 Onse amenewo anadziphatikana pa cigwa ca Sidimu (pamenepo ndi pa nyanja yamcere).
4 Zaka khumi ndi ziwiri iwo anamtumikira Kedorelaomere, caka cakhumi ndi citatu anapanduka,
5 Caka cakhumi ndicinai ndipo anadza Kedorelaomere ndi mafumu amene anali naye, nawakantha Arefai m'Aseteroti-kamaimu, ndi Azuzi m'Hamu, ndi Aemi m'Savekiriataimu,
6 ndi Ahori pa phiri lao Seiri kufikira ku Eliparana, kumene kuli pacipululu.
7 Ndipo anabwera nafika ku Eni-Misipati (ku meneko ndi ku Kadese), nakantha dziko lonse la Aamaleki, ndiponse Aamori amene akhala m'Hazezoni-tamara.
8 Ndipo anaturuka mfumu ya Sodomu, ndi ya Gomora, ndi mfumu ya Adima, ndi mfumu ya Zeboimu, ndi mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zoari) ndipo anawathira nkhondo m'cigwa ca Sidimu
9 ndi Kedorelaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu ndi Amarafele mfumu ya Sinara, ndi Arioki mfumu ya Elasara; mafumu anai kugwirana ndi asanu.