13 Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, Bwanji anaseka Sara, kuti, Kodi ndidzabala ine ndithu, ine amene ndakalamba?
14 Kodi ciripo cinthu comlaka Yehova? Pa nthawi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yace, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.
15 Koma Sara anakana, nati, Sindinasekai; cifukwa anaopa, Ndipo anati, lai; koma unaseka.
16 Ndipo anthuwo anauka kucokera kumeneko nayang'ana ku Sodomu; ndipo Abrahamu ananka nao kuwaperekeza.
17 Ndipo Yehova adati, Kodi ndidzabisira Abrahamu cimene ndicita?
18 Pakuti Abrahamu adzakhala ndithu wamkuru ndi wamphamvu, ndipo mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsika mwa iye?
19 Cifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ace ndi banja lace la pambuyo pace, kuti asunge njira ya Yehova, kucita cilungamo ndi ciweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu comwe anamnenera iye.