20 Ndipo anati Yehova, Popeza kulira kwa Sodomu ndi Gomora kuli kwakukuru, ndipo popeza kucimwa kwao kuli kulemera ndithu,
21 ndidzatsikatu ndikaone ngati anacita monse monga kulira kwace kumene kunandifikira: ngati sanatero ndidzadziwa.
22 Ndipo anthuwo anatembenuka nacoka kumeneko, napita kunka ku Sodomu. Koma Abrahamu anaimabe pamaso pa Yehova.
23 Ndipo Abrahamu anayandikira nati, Kodi mudzaononga olungama pamodzi ndi oipa?
24 Kapena alipo olungama makumi asanu m'kati mwa mudzi; kodi mudzaononga, simudzasiya malowa cifukwa ca olungama makumi asanu ali momwemo?
25 Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzacita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?
26 Ndipo anati Yehova, Ndikapeza m'Sodomu olungama makumi asanu m'kati mwa mudzi, ndidzasiya malo onse cifukwa ca iwo.