1 Ndipo anadza ku Sodomu madzulo amithenga awiri; ndipo Loti anakhala pa cipata ca Sodomu, ndipo Loti anaona iwo, nauka kuti akakomane nao, ndipo anaweramitsa pansi nkhope yace.
2 Ndipo anati, Taonanitu, ambuye anga, tembenukanitu, kulowa m'nyumba mwa kapolo wanu, mugone usiku wonse, mutsuke mapazi anu, ndipo mudzalawira m'mawa kunka ulendo wanu. Ndipo anati, lai; koma tigone m'khwalalamu usiku wonse.
3 Ndipo anawaumiriza iwo ndithu: ndipo anapatukira kwa iye, nalowa m'nyumba mwace; ndipo anawakonzera iwo madyerero, naphika mikate yopanda cotupitsa, ndipo anadya,
4 Koma asanagone, anthu a m'mudzimo anthu a Sodomu, anazinga nyumba, anyamata ndi okalamba, anthu onse a m'mbali zonse;
5 ndipo anamuitana Loti, nati kwa iye, Ali kuti anthu amene anadza kwa iwe madzulo ano, utiturutsire iwo kuti tiwadziwe.
6 Ndipo Loti anaturukira kwa iwo pakhomo, natseka cambuyo pakhomo pace.
7 Ndipo anati, Abale anga, musacitetu koipa kotere.