22 Fulumira, thawira kumeneko; pakuti sindithai kucita kanthu usadafike kumeneko. Cifukwa cace anacha dzina la mudziwo Zoari.
23 Ndipo dzuwa lidakwera pa dziko pamene Loti anafika ku Zoari.
24 Ndipo Yehova anabvumbitsa pa Sodomu ndi pa Gomora miyala ya sulfure ndi mota kuturuka kwa Mulungu kumwamba;
25 ndipo anaononga midziyo, ndi cigwa conse, ndi onse akukhala m'midzimo, ndi zimene zimera panthaka.
26 Koma mkazi wace anaceuka ali pambuyo pace pa Loti, nasanduka mwala wamcere.
27 Ndipo Abrahamu analawiram'mamawa kunka kumalo kumene anaima pamaso pa Yehova:
28 ndipo anayang'anira ku Sodomu ndi ku Gomora ndi ku dziko lonse la cigwa, ndipo anapenya, taonanitu, utsi wa dzikolo unakwera, monga utsi wa ng'anjo.