1 Ndipo zinatha kupangidwa zakumwamba ndi dziko lapansi, ndi khamu lao lonse.
2 Tsiku lacisanu ndi ciwiri Mulungu anamariza nchito yonse anaipanga; ndipo anapuma tsiku lacisanu ndi ciwiri ku nchito yace yonse.
3 Mulungu ndipo anadalitsa tsiku lacisanu ndi ciwiri, naliyeretsa limenelo: cifukwa limenelo ada puma ku nchito yace yonse imene Mulungu anailenga ndi kupanga.
4 Imeneyo ndiyo mibadwo yao ya zakumwamba ndi dziko lapansi, pamene zinalengedwa, tsiku lomwe Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zakumwamba.
5 Ndi zomera zonse za m'munda zisanakhale m'dziko lapansi, ndiponso matherere onse a m'munda asanamere; cifukwa Yehova Mulungu sanabvumbitsire mvula pa dziko lapansi, ndipo panalibe munthu wakulima nthaka;