4 Imeneyo ndiyo mibadwo yao ya zakumwamba ndi dziko lapansi, pamene zinalengedwa, tsiku lomwe Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zakumwamba.
5 Ndi zomera zonse za m'munda zisanakhale m'dziko lapansi, ndiponso matherere onse a m'munda asanamere; cifukwa Yehova Mulungu sanabvumbitsire mvula pa dziko lapansi, ndipo panalibe munthu wakulima nthaka;
6 kama inakwera nkhungu yoturuka pa dziko lapansi, niithirira ponse pamwamba pa nthaka.
7 Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwace; munthuyo nakhala wamoyo.
8 Ndipo Yehova Mulungu anabzala m'munda ku Edene cakum'mawa; momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo.
9 Ndipo Yehova Mulungu anameretsa m'nthaka mitengo yonse yokoma m'maso ndi yabwino kudya; ndiponso mtengo wa moyo pakati pa mundapo, ndi mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa.
10 Ndipo unaturuka m'Edene mtsinje wakuthirira m'mundamo, m'menemo ndipo unalekana nucita miyendo inai.