3 Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa namanga buru wace, natengako anyamata ace awiri pamodzi naye, ndi Isake mwana wace, nawaza nkhuni za nsembe, nauka, nanka kumalo komwe Mulungu anamuuza iye,
4 Tsiku lacitatu Abrahamu anatukula maso ace naona malowo patari.
5 Ndipo Abrahamu anati kwa anyamata ace, Khalani kuno ndi buru, ine ndi mwanayu tinka uko, ndipo tikapemphera ndi kubweranso kwa inu.
6 Ndipo Abrahamu anatenga nkhuni za nsembe yopsereza, nazisenzetsa Isake mwana wace; natenga mota m'dzanja lace ndi mpeni; nayenda pamodzi onse awiri.
7 Ndipo Isake ananena ndi Abrahamu atate wace, nati, Atate wanga; ndipo iye anati, Ndine pano, mwana wanga. Ndipo anati, Taonani moto ndi nkhuni; koma mwana wa nkhosa wa nsembe yopsereza ali kuti?
8 Ndipo Abrahamu anati, Mwana wanga, Mulungu adzadzifunira yekha mwana wa nkhosa wa nsembe yopsereza; nayenda pamodzi onse awiri.
9 Ndipo anafika kumalo komwe Mulungu anamuuza iye; ndipo Abrahamu anamanga guwa la nsembe nakonza nkhuni, namanga Isake mwana wace, namuika iye pa guwa la nsembe pamwamba pa nkhuni.