1 Ndipo Abrahamu anatenga mkazi wina dzina lace Ketura.
2 Ndipo anambalira iye Zimerani ndi Yokesani ndi Medani, ndi Midyani, ndi Yisebaki, ndi Sua.
3 Ndipo Yokesani anabala Seba, ndi Dedani. Ana a Dedani ndi Aasuri, ndi Aletusi, ndi Aleumi.
4 Ana a Midyani: Efa, ndi Efere, ndi Hanoki, ndi Abida, ndi Elida. Onse amenewa ndi ana a Ketura.
5 Ndipo Abrahamu amwali anampatsa Isake zonse anali nazo.