10 munda umene anagula Abrahamu kwa ana a Heti: pamenepo anamuika Abrahamu ndi Sara mkazi wace.
11 Ndipo panali atafa Abrahamu, Mulungu anamdalitsa Isake mwana wace; ndipo Isake anakhala pa Beere-lahai-roi.
12 Mibadwo ya Ismayeli mwana wamwamuna wace wa Abrahamu, amene Hagara M-aigupto mdzakazi wa Sara anambalira Abrahamu ndi iyi:
13 ndipo maina a ana a Ismayeli, maina ao m'mibadwo yao ndi awa: woyamba wa Ismayeli ndi Nebayoti; ndi Kedara, ndi Abideele, ndi Mibisamu,
14 ndi Misima, ndi Duma; ndi Masa;
15 ndi Hadada, ndi Tema, ndi Yeturi, ndi Nafisi, ndi Kedema;
16 ana a Ismayeli ndi awa: maina ao m'midzi yao, m'misasa yao ndi awa: akaronga khumi ndi awiri m'mitundu yao.