7 Masiku a zaka za moyo wace wa Abrahamu amene anakhala ndi moyo ndiwo zaka zana limodzi, kudza makumi asanu ndi limodzi, kudza khumi ndi zisanu.
8 Ndipo Abrahamu anamwalira, nafa m'ukalamba wace wabwino, nkhalamba ya zaka zambiri; natengedwa akhale ndi a mtundu wace.
9 Ndipo ana ace Isake ndi Ismayeli anamuika iye m'phanga la Makipela, m'munda wa Efroni mwana wace wa Zohari Mhiti, umene uli patsogolo pa Mamre;
10 munda umene anagula Abrahamu kwa ana a Heti: pamenepo anamuika Abrahamu ndi Sara mkazi wace.
11 Ndipo panali atafa Abrahamu, Mulungu anamdalitsa Isake mwana wace; ndipo Isake anakhala pa Beere-lahai-roi.
12 Mibadwo ya Ismayeli mwana wamwamuna wace wa Abrahamu, amene Hagara M-aigupto mdzakazi wa Sara anambalira Abrahamu ndi iyi:
13 ndipo maina a ana a Ismayeli, maina ao m'mibadwo yao ndi awa: woyamba wa Ismayeli ndi Nebayoti; ndi Kedara, ndi Abideele, ndi Mibisamu,