17 Ndipo Isake anacoka kumeneko, namanga hema wace m'cigwa ca Gerari, nakhala kumeneko.
18 Ndipo Isake anafukulanso zitsime za madzi, anazikumba masiku a Abrahamu atate wace; cifukwa kuti Afilisti anazitseka atafa Abrahamu: ndipo anazicha maina monga maina omwe anazicha atate wace.
19 Ndipo anyamata a Isake anakumba m'cigwa, napeza kumeneko citsime ca madzi otumphuka.
20 Ndipo abusa a Gerari anakangana ndi abusa a Isake kuti, Madzi ndi athu; ndipo anacha dzina la citsimeco Eseke: cifukwa anakangana nave.
21 Ndipo anakumbanso citsime cina, ndipo anakangana naconso; nacha dzina lace Sitina.
22 Ndipo anacoka kumeneko nakumba citsime cina; koma sanakangana naco cimeneco; ndipo anacha dzina lace Rehoboti; ndipo anati, Cifukwa kuti tsopano Yehova anatipatsa ife malo, ndipo tidzabalana m'dziko muno.
23 Ndipo anacoka kumeneko nakwera kunka ku Beereseba,