5 cifukwa kuti Abrahamu anamvera mau anga, nasunga cilangizo canga, ndi maweruziro anga, ndi malemba anga ndi malamulo anga.
6 Ndipo Isake anakhala m'Gerari;
7 ndipo anthu a kumeneko anamfunsa iye za mkazi wace; ndipo iye anati, diye mlongowanga: cifukwa kuti anaopa kunena, Mkazi wanga; anati, anthu a kumeneko angandiphe ine cifukwa ca Rebeka; popeza anali wokongola pakumuona.
8 Ndipo panali atakhala komwe masiku ambiri, Abimeleke mfumu ya Afilisti, anayang'ana kunja kwa zenera, napenya, taona, Isake analinkuseka ndi Rebeka mkazi wace.
9 Ndipo Abimeleke anamuitana Isake nati, Taona, uyo ndi mkazi wako ndithu: kodi bwanji unati, Ndiye mlongo wanga? Ndipo Isake anati kwa iye, Cifukwa ndinati, Ndingafe cifukwa ca iye.
10 Ndipo Abimeleke anati, Nciani cimeneci waticitira ife? panatsala pang'ono ena a anthu akadagona naye mkazi wako, ndipo ukadaticimwitsa ife:
11 Ndipo Abimeleke anauza anthu ace, nati, Ali yense amene akhudza mwamuna uyo kapena mkazi wace, zoonatu adzaphedwa.