1 Ndipo Yakobo ananka ulendo wace, nafika ku dziko la anthu a kum'mawa.
2 Ndipo anayang'ana, taonani, citsime m'dambo, ndipo, taonani, magulu atatu a nkhosa alinkugona kumeneko: pakuti pacitsimepo anamwetsa nkhosa; ndipo mwala wa pakamwa pa citsime unali waukuru.
3 Kumeneko ndipo zinasonkhana zoweta zonse: ndipo anagubuduza mwala kuucotsa pakamwa pa citsime, namwetsa nkhosa, naikanso mwala pakamwa pa citsime pamalo pace.
4 Ndipo anati Yakobo kwa iwo, Abale anga, ndinu a kuti inu? nati, Ndife a ku Harana.
5 Ndipo anati kwa iwo, Kodi mumdziwa Labani mwana wace wa Nahori? nati, Timdziwa.
6 Ndipo anati kwa iwo, Kodi ali bwino? nati, Ali bwino: taonani, Rakele mwana wace wamkazi alinkudza nazo nkhosa.