3 Kumeneko ndipo zinasonkhana zoweta zonse: ndipo anagubuduza mwala kuucotsa pakamwa pa citsime, namwetsa nkhosa, naikanso mwala pakamwa pa citsime pamalo pace.
4 Ndipo anati Yakobo kwa iwo, Abale anga, ndinu a kuti inu? nati, Ndife a ku Harana.
5 Ndipo anati kwa iwo, Kodi mumdziwa Labani mwana wace wa Nahori? nati, Timdziwa.
6 Ndipo anati kwa iwo, Kodi ali bwino? nati, Ali bwino: taonani, Rakele mwana wace wamkazi alinkudza nazo nkhosa.
7 Ndipo iye anati, Taonani, kukali msana, si nthawi yosonkhanitsa zoweta; mwetsani nkhosa, pitani, kadyetseni.
8 Ndipo anati, Sitingathe, koma zitasonkhana ziweto zonse, ndipo atagubuduza mwala kuucotsa pakamwa pa citsime ndiko; pamenepo ndipo tizimwetsa nkhosa.
9 Ali cilankhulire nao, anafika Rakele ndi nkhosa za atate wace, cifukwa anaziweta.