7 Ndipo iye anati, Taonani, kukali msana, si nthawi yosonkhanitsa zoweta; mwetsani nkhosa, pitani, kadyetseni.
8 Ndipo anati, Sitingathe, koma zitasonkhana ziweto zonse, ndipo atagubuduza mwala kuucotsa pakamwa pa citsime ndiko; pamenepo ndipo tizimwetsa nkhosa.
9 Ali cilankhulire nao, anafika Rakele ndi nkhosa za atate wace, cifukwa anaziweta.
10 Ndipo panali pamene Yakobo anaona Rakele, mwana wamkazi wa Labani, mlongo wace wa amace, ndi nkhosa za Labani mlongo wace wa amace, Yakobo anayandikira nagubuduza kuucotsa mwala pacitsime, nazimwetsa zoweta za Labani, mlongo wace wa amace.
11 Ndipo Yakobo anampsompsona Rakele nakweza mau ace, nalira.
12 Ndipo Yakobo anamuuza Rakele kuti iye ndiye mbalewace wa atate wace, kuti ndiye mwana wace wa Rebeka, ndipo Rakele anathamanga nakauza atate wace.
13 Ndipo panali pamene Labani anamva mbiri ya Yakobo mwana wa mlongo wace, iye anathamangira kukakomana naye namfungatira, nampsompsona, namlowetsa m'nyumba mwace. Ndipo iye anamfotokozera Labani zinthu zonsezo.