19 Ndipo Leya anatenganso pakati nambalira Yakobo mwana wamwamuna wacisanu ndi cimodzi.
20 Ndipo Leya anati, Mulungu anandipatsa ine mphatso yabwino; tsopane mwamuna wanga adzakhala ndi ine, cifukwa ndambalira iye ana amuna asanu ndi mmodzi; ndipo anamucha dzina lace Zebuloni.
21 Pambuyo pace ndipo anabala mwana wamkazi, namucha dzina lace Dina.
22 Ndipo Mulungu anakumbukila Rakele, ndipo Mulungu anamvera iye, natsegula m'mimba mwace.
23 Ndipo anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, nati, Mulungu wacotsa manyazi anga;
24 namucha dzina lace Yosefe; ndipo anati, Yehova anandionjezera ine mwana wamwamuna wina.
25 Ndipo panali pamene Rakele anabala Yosefe, Yakobo anati kwa Labani, Undisudzule ine ndinke kwathu ku dziko langa.