24 namucha dzina lace Yosefe; ndipo anati, Yehova anandionjezera ine mwana wamwamuna wina.
25 Ndipo panali pamene Rakele anabala Yosefe, Yakobo anati kwa Labani, Undisudzule ine ndinke kwathu ku dziko langa.
26 Undipatse ine akazi anga ndi ana anga cifukwa ca iwowa ndakutumikira iwe, ndimuke: cifukwa udziwa iwe nchito imene ndinakugwirira iwe.
27 Ndipo Labani anati kwa iye, Ngatitu ndikapeza ufulu pamaso pako, ukhale, cifukwa ndazindikira kuti Yehova wandidalitsa ine cifukwa ca iwe.
28 Ndipo iye anati, Undipangire ine malipiro ako, ndipo ndidzakupatsa.
29 Ndipo iye anati kwa Labani, Udziwa iwe comwe ndakutumikira iwe ndi comwe zacita zoweta zako ndi ine.
30 Cifukwa ndisadafike ine, iwe unali nazo zowerengeka, ndipo zacuruka zambirimbiri; Yehova wakudalitsa iwe kuli konse ndinayendako: tsopano ndidzamanga liti banja langa?