36 Ndipo anakwiya Yakobo namkalipira Labani: ndipo Yakobo anayankha nati kwa Labani, Kodi ndacimwa ciani? ucimo wanga nguti, kuti unanditsatatsata ine pambuyo panga?
37 Pakuti wafunafuna monse ndiri nazo, kodi wapeza ciani pa zinthu za m'nyumba mwako? Tafika naco apa pa abale anga ndi ako, kuti aweruze pa ife tonse awiri.
38 Zaka makumi awiriwo ndakhala nawe, nkhosa ndi mbuzi zako zazikazi sizinapoloze, ndi abira a zoweta zako sindinadye.
39 Cimene cinazomoledwa ndi cirombo sindinacitengere kwa iwe; ndekha ndinalipira; pa dzanja langa unacifuna, cingakhale cobedwa kapena pausiku kapena pausana.
40 Cotero ndinakhala; usana ludzu linakomola ine, usiku cisanu; tulo tanga tinacoka m'maso mwanga.
41 Ndinakhala cotere zaka makumi awiri m'nyumba mwako; zaka khumi ndi zinai ndinakutumikira iwe cifukwa ca ana ako akazi awiri, ndi zaka zisanu ndi cimodzi cifukwa ca zoweta zako; wasintha malipiro anga kakhumi.
42 Mulungu wa atate wanga, Mulungu wa Abrahamu, ndi Kuopsa kwa Isake zikadapanda kukhala ndi ine, ukadandicotsa ine wopanda kanthu m'manja. Mulungu anakuona kusauka kwanga, ndi nchito ya manja anga, ndipo anadzudzula iwe usiku walero.