2 Pamene Yakobo anawaona anati, Ili ndi khamu la Mulungu: ndipo anacha pamenepo dzina lace Mahanaimu.
3 Ndipo Yakobo anatumiza amithenga patsogolo pace kwa Esau mkuru wace, ku dziko la Seiri, ku dera la ku Edomu.
4 Ndipo anauza iwo kuti, Mukanene cotere kwa mbuyanga Esau: Atero Yakobo kapolo wako, ndakhala pamodzi naye Labani, ndipo ndakhalabe kufikira tsopano line:
5 ndipo ndiri nazo ng'ombe ndi aburu, ndi zoweta ndi akapolo ndi adzakazi, ndipo ndatumiza kukuuza mbuyanga kuti ndipeze ufulu pamaso pako.
6 Ndipo amithenga anabwera kwa Yakobo kuti, Tidafika kwa mbale wanu Esau, ndipo iyenso alinkudza kukomana nanu, ndipo ali nao anthu mazana anai.
7 Ndipo Yakobo anaopa kwambiri, nabvutidwa; ndipo anagawa anthu anali nao ndi nkhosa ndi zoweta, ndi ngamila, zikhale makamu awiri;
8 ndipo anati, Akafika Esau pa khamu limodzi nalikantha, linalo lotsala lidzapulumuka.