16 Ndipo Esau anabwera tsiku lomwelo kunka ku Seiri.
17 Ndipo Yakobo anankabe ulendo wace ku Sukoti, namanga nyumba yace pamenepo, namanga makola a zoweta zace: cifukwa cace dzina lace la kumeneko ndi Sukoti.
18 Ndipo Yakobo anafika ndi mtendere ku mudzi wa Sekemu umene uli m'dziko la Kanani, pamene anacokera ku Padanaramu; namanga tsasa pandunji pa mudzipo.
19 Ndipo anagula ndi ndalama zana limodzi dera la munda kumeneko anamanga bema wace, pa dzanja la ana ace a Hamori atate wace wa Sekemu.
20 Ndipo anamanga pamenepo guwa la nsembe, nacha pamenepo EleloheIsrayeli.