1 Mibadwo ya Esau (ndiye Edomu) ndi iyi:
2 Esau anatenga akazi ace a ana akazi a m'Kanani: Ada mwana wamkazi wa Eloni Mhiti, ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibeoni Mhivi;
3 ndi Basemati mwana wamkazi wa lsmayeli, mlongo wace wa Nabayoti.
4 Ndipo Ada anambalira Esau Elifazi; ndipo Basemati anabala Reueli;
5 ndipo Oholibama anabala Jeusi, ndi Jalamu, ndi Kora; amenewa ndi ana amuna a Esau, amene anambadwira m'dziko la Kanani.
6 Ndipo Esau anatenga akazi ace, ndi ana ace amuna, ndi ana ace akazi, ndi anthu onse a m'banja mwace, ndi ng'ombe zace, ndi zoweta zace, ndi zonse anali nazo anasonkhanitsa m'dziko la Kanani; ndipo ananka ku dziko losiyana patari ndi Yakobo mphwace.