1 Ndipo anatsika naye Yosefe kunka ku Aigupto; ndipo Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda, Maigupto, anamgula iye m'manja mwa Aismayeli amene anatsika naye kunka iumeneko.
2 Ndipo Yehova anali ndi Yosefe; ndipo iye anali wolemeralemera; nakhala m'nyumba ya mbuyace M-aigupto.
3 Ndipo mbuyace anaona kuti Yehova anali ndi iye, ndi kuti Yehova anamlemereza m'dzanja lace zonse anazicita.
4 Ndipo Yosefe anapeza ufulu pamaso pace, ndipo anamtumikira iye; ndipo anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yace, naika m'manja mwace zonse anali nazo.
5 Ndipo panali ciyambire anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yace, ndi pa zace zonse, Yehova anadalitsa nyumba ya M-aigupto cifukwa ca Yosefe; ndipo mdalitso wa Yehova unali pa zace zonse, m'nyumba ndi m'munda.
6 Ndipo iye anasiya zace zonse m'manja a Yosefe; osadziwa comwe anali naco, koma cakudya cimene anadya. Ndipo Yosefe anali wokoma thupi ndi wokongola.
7 Ndipo panali zitapita izi, kuti mkazi wa mbuyace anamyang'anira maso Yosefe: ndipo mkaziyo anati, Gona ndi ine.