4 Ndipo kazembe wa alonda anapereka iwo kwa Yosefe, ndipo iye anawatumikira iwo: ndipo anakhala nthawi mosungidwamo.
5 Ndipo analota maloto onse awiri, yense lata lace, usiku umodzi, yense monga mwa kumasulira kwa loto lace, wopereka cikho ndi wophika mkate wa mfumu ya Aigupto, amene anamangidwa m'kaidi.
6 Ndipo Yosefe analowa kwa iwo m'mawa, nawaona iwo, taonani, anali oziya.
7 Ndipo anafunsa akuru a Farao osungidwa naye m'nyumba ya mbuyace, kuti, Nkhope zanu zagwa bwanji lero?
8 Ndipo iwo anati kwa iye, Ife talota maloto, ndipo tiribe wotimasulira. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Kodi Mwini kumasulira si ndiye Mulungu? Mundifotokozeretu.
9 Ndipo wopereka cikho wamkuru anafotokozera Yosefe loto lace, nati kwa iye, M'kulota kwanga, taona, mpesa unali pamaso panga:
10 ndipo m'mpesamo munali nthambi zitatu: ndipo unali wonga unaphuka, ndipo maluwa ace anaphuka; nabala matsamvu ace mphesa zakuca: