5 Koma mukapanda kumtuma iye sititsika; pakuti munthu uja anati kwa ife, Simudzaona nkhope yanga, ngati mphwanu sali ndi inu.
6 Ndipo Israyeli anati, Cifukwa ninji munandicitira ine coipa cotero kuti munamuuza munthuyo muli ndi mphwanu?
7 Ndipo iwo anati, Munthuyo anafunsitsa za ife, ndi za abale athu, kuti, Atate wanu alipo? Kodi muli ndi mphwanu? ndipo tinamfotokozera iye monga mwa mau amenewo: ngati tinadziwa kuti iye adzati, Idzani naye mphwanu?
8 Ndipo Yuda anati kwa atate wace Israyeli, Mumtume mnyamata pamodzi ndi ine ndipo ife tidzanyamuka ndi kupita; kuti tikhale ndi moyo tisafe, ife ndi inu ndi ana athu ang'ono.
9 Ine ndidzakhala cikole, pa manja anga mudzamfunsa: ndikapanda kumbwezera kwa inu ndi kumuimitsa pamaso panu, cifukwa cace cidzakhala pa ine masiku onse:
10 pakuti tikadaleka kucedwa mwenzi tsopano titabwera kawiri.
11 Ndipo Israyeli atate wao anati kwa iwo, Ngati comweco tsopano citani ici: tengani zipatso za m'dziko muno m'zotengera zanu, mumtengere munthu uja mphatso, mafuta a mankhwala pang'ono, ndi uci pang'ono, zonunkhira ndi mure, ndi mfula, ndi katungurume;