24 Ndipo panali titakwera kunka kwa kapolo wanus atate, wanga, tinamfotokozera iye mau a mbuyanga.
25 Ndipo atate wathu anati, Mupitenso mutigulire ife cakudya pang'ono.
26 Ndipo ife tinati, Sitingathe kupita; mphwathu wamng'ono akakhala ndi ife, pamenepo tidzapita; pakuti sitingaone nkhope ya munthu uja, mphwathu wamng'ono akapanda kukhala ndi ife.
27 Ndipo kapolo wanu atate wanga anati kwa ife, Inu mudziwa kuti mkazi wanga anandibalira ine ana amuna awiri;
28 wina anaturuka kwa ine ndipo ndinati, Zoonatu, wakadzulidwa; ndipo sindidzamuonanso iye;
29 ndipo ngati mukandicotsera ameneyonso, ndipo ngati cimgwera coipa, mudzanditsitsira ndi cisoni imvi zanga kumanda.
30 Cifukwa cace ndikafika kwa kapolo wanu atate wanga, ndipo mnyamata akapanda kukhala ndi ife; popeza moyo wace uli womangidwa ndi moyo wa mnyamatayo;