19 tiferenji pamaso panu, ife ndi dziko lathu? mutigule ife ndi dziko lathu ndi cakudya, ndipo ife ndi dziko lathu tidzakhala akapolo a Farao; ndipo mutipatse ife mbeu, kuti tikhale ndi moyo, tisafe, ndi kuti dziko lisakhale labwinja.
20 Ndipo Yosefe anamgulira Farao dziko lonse la Aigupto, cifukwa Aaigupto anagulitsa yense munda wace, cifukwa njala inakula pa iwo; ndipo dziko linakhala la Farao.
21 Tsono anthu, anasunthira iwo ku midzi kucokera kumphepete kwa malire a Aigupto kufikira kumphepete kwina kwace.
22 Koma dziko la ansembe lokha sanagule, cifukwa ansembe analandira gawo lao kwa Farao, nadya gawolo anawapatsa Farao; cifukwa cace sanagulitsa dziko lao.
23 Ndipo Yosefe anati kwa anthu, Taonani, ndamgulira Farao inu ndi dziko lanu lero lomwe, taonani, mbeu zanu sizi, mubzale m'dziko.
24 Ndipo padzakhala pakukunkha, muzipatsa limodzi la mwa magawo asanu kwa Farao, koma magawo anai ndi anu, mbeu za munda, ndi za cakudya canu, ndi ca ana anu ndi mabanja anu.
25 Ndipo iwo anati, Watipulumutsa miyoyo yathu; tipeze ufulu pamaso pa mbuyanga, ndipo tidzakhala akapolo a Farao.