4 Nati kwa Farao, Tafika kuti tikhale m'dzikomo; popeza palibe podyetsa zoweta za akapolo anu; pakuti njala yakula m'dziko la Kanani. Mulole tsopano akapolo anu akhale m'dziko la Goseni.
5 Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Atate wako ndi abale ako afika kwa iwe;
6 dziko la Aigupto liri pamaso pako: uwakhazike atate wako ndi abale ako pa dera lokometsetsa la dziko; akhale m'dziko la Goseni; ndipo ngati udziwa anthu anzeru a mwa iwo, uwaike iwo ayang'anire ng'ombe zanga.
7 Ndipo Yosefe analowa naye Yakobo atate wace, namuika iye pamaso pa Farao; ndipo Yakobo anamdalitsa Farao.
8 Ndipo Farao anati kwa Yakobo, Masiku a zaka za moyo wanu ndi angati?
9 Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo angam'masikua ulendowao.
10 Ndipo Yakobo anamdalitsa Farao, naturuka pamaso pa Farao.