1 Ndipo panali zitapita izi, anthu anati kwa Yosefe, Taonani, atate wanu wadwala: ndipo iye anatenga ana ace amuna awiri, Manase ndi Efraimu, apite naye.
2 Ndipo anthu anamuuza Yakobo nati, Taonani, mwana wanu Yosefe alinkudza kwa inu; ndipo Yakobo anadzilimbitsa, nakhala tsonga pakama.
3 Ndipo Yakobo anati kwa Yosefe, a Mulungu Wamphamvuyonse anaonekera kwa ine pa Luzi m'dziko la Kanani nandidalitsa ine, nati kwa ine,
4 Taona, ndidzakubalitsa iwe, ndidzakucurukitsa iwe, ndidzakusandutsa iwe khamu la anthu a mitundu; ndipo ndidzapatsa mbeu yako ya pambuyo pako dziko ili likhale laolao cikhalire.