3 Ndipo Yakobo anati kwa Yosefe, a Mulungu Wamphamvuyonse anaonekera kwa ine pa Luzi m'dziko la Kanani nandidalitsa ine, nati kwa ine,
4 Taona, ndidzakubalitsa iwe, ndidzakucurukitsa iwe, ndidzakusandutsa iwe khamu la anthu a mitundu; ndipo ndidzapatsa mbeu yako ya pambuyo pako dziko ili likhale laolao cikhalire.
5 Tsopano ana ako amuna awiri, amene anakubadwira iwe m'dziko la Aigupto, ndisanadze kwa iwe ku Aigupto, ndiwo anga; Efraimu ndi Manase, monga Rubeni ndi Simeoni, ndiwo anga.
6 Koma obala iwe udzawabala pambuyo pao, ndiwo ako; awaphe dzina la abale ao m'colowa cao.
7 Tsono ine, pamene ndinacokera ku Padani, Rakele anamwalira pambali panga m'dziko la Kanani m'njira, itatsala nthawi yaing'ono tisadafike ku Efrati; ndipo ndidamuika iye pamenepo pa njira ya ku Efrati (ndiwo Betelehemu).
8 Ndipo Israyeli anayang'ana ana amuna a Yosefe, nati, Ndani awa?
9 Ndipo Yosefe anati kwa atate wace, Amenewa ndi ana anga, amene Mulungu wandipatsa ine pano. Ndipo iye anati, Udze naotu kwa ine, ndipo ndidzawadalitsa.