1 Ndipo Yakobo anaitana ana ace amuna, nati, Sonkhanani inu, kuti ndikuuzeni inu cimene cidzakugwerani inu masiku akudzawo.
2 Sonkhanani, tamvani, ana amuna a Yakobo:Tamverani Israyeli atate wanu:
3 Rubeni, ndiwe woyamba wanga, mphamvu yanga ndi ciyambi ca mphamvu yanga;Ulemu wopambana, ndi mphamvu yopambana.
4 Wobwabwada ngati madzi; sudzapambana;Cifukwa unakwera pa kama wa atate wako;Pamenepo unaipitsapo; anakwera paja ndigonapo.