1 Ndipo Yakobo anaitana ana ace amuna, nati, Sonkhanani inu, kuti ndikuuzeni inu cimene cidzakugwerani inu masiku akudzawo.
2 Sonkhanani, tamvani, ana amuna a Yakobo:Tamverani Israyeli atate wanu:
3 Rubeni, ndiwe woyamba wanga, mphamvu yanga ndi ciyambi ca mphamvu yanga;Ulemu wopambana, ndi mphamvu yopambana.
4 Wobwabwada ngati madzi; sudzapambana;Cifukwa unakwera pa kama wa atate wako;Pamenepo unaipitsapo; anakwera paja ndigonapo.
5 Simeoni ndi Levi ndiwo abale;Zida za mphulupulu ndizo malupanga ao.
6 Mtima wangawe, usalowe mu ciungwe cao;Ulemerero wanga, usadziphatike pa masonkhano ao;Cifukwa m'kukwiya kwao anapha munthu,M'kufuna kwao anapundula ng'ombe.