17 Dani adzakhala njoka m'khwalala,Songo panjira,Imene iluma zitende za kavalo,Kuti womkwera wace agwe cambuyo.
18 Ndadikira cipulumutso canu, Yehova.
19 Ndi Gadi, acifwamba adzampsinja iye;Koma iye adzapsinja pa citende cao.
20 Ndi Aseri, cakudya cace ndico mafuta,Ndipo adzapereka zolongosoka zacifumu.
21 Nafitali ndi nswala yomasuka;Apatsa mau abwino.
22 Yosefe ndi nthambi yobala,Nthambi yobala pambali pa kasupe;Nthambi zace ziyangayanga palinga.
23 Eni uta anabvutitsa iye kwambiri,Namponyera iye, namzunza: