19 Ndi Gadi, acifwamba adzampsinja iye;Koma iye adzapsinja pa citende cao.
20 Ndi Aseri, cakudya cace ndico mafuta,Ndipo adzapereka zolongosoka zacifumu.
21 Nafitali ndi nswala yomasuka;Apatsa mau abwino.
22 Yosefe ndi nthambi yobala,Nthambi yobala pambali pa kasupe;Nthambi zace ziyangayanga palinga.
23 Eni uta anabvutitsa iye kwambiri,Namponyera iye, namzunza:
24 Koma uta wace unakhala wamphamvu,Ndi mikono ya manja ace inalimbitsidwaNdi manja a Wamphamvu wa Yakobo.(Kucokera kumeneko ndi mbusa, mwala wa Israyeli,)
25 Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe,Ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iweNdi madalitso a Kumwamba,Madalitso a madzi akuya akukhala pansi,Madalitso a mabere, ndi a mimba.