22 Yosefe ndi nthambi yobala,Nthambi yobala pambali pa kasupe;Nthambi zace ziyangayanga palinga.
23 Eni uta anabvutitsa iye kwambiri,Namponyera iye, namzunza:
24 Koma uta wace unakhala wamphamvu,Ndi mikono ya manja ace inalimbitsidwaNdi manja a Wamphamvu wa Yakobo.(Kucokera kumeneko ndi mbusa, mwala wa Israyeli,)
25 Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe,Ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iweNdi madalitso a Kumwamba,Madalitso a madzi akuya akukhala pansi,Madalitso a mabere, ndi a mimba.
26 Madalitso a atate wakoApambana mphamvu ndi madalitso a makolo anga,Kufikira ku malekezero a patari a mapiri a cikhalire;Adzakhala pa mutu wa Yosefe,Ndi pakati pa mutu wa iye amene ali wolekanitsidwa ndi abale ace.
27 Benjamini ndiye mmbulu wakulusalusa;M'mamawa adzadya comotola,Madzulo adzagawa zofunkha.
28 Awa onse ndiwo mafuko khumi ndi awiri a Israyeli: izo ndizo zomwe ananena kwa iwo atate wao nawadalitsa; yense monga mdalitso wace anawadalitsa.